Pitani ku nkhani yake

AZERBAIJAN

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Malamulo a m’dziko la Azerbaijan amalola anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo kuti azipatsidwa mwayi wogwira ntchito zina. Komabe dzikoli silinayambe kutsatira lamulo loti anthu oterewa azipatsidwa ntchito zina. Chifukwa cha zimenezi a Mboni za Yehova amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo ndiponso chifukwa cha zimene amakhulupirira amazunzidwa komanso kuikidwa m’ndende.

Boma la Azerbaijan Likulephera Kukwaniritsa Udindo Wake

Dziko la Azerbaijan linalowa m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya m’chaka cha 1996. Mogwirizana ndi malamulo a bungweli, dzikoli linavomereza kuti: (1) pambuyo pa zaka ziwiri lidzakhala ndi lamulo lovomereza anthu amene safuna kulowa usilikali kuti akhoza kugwira ntchito zina, (2) kuti lidzamasula anthu onse amene anamangidwa atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo komanso (3) kuti lidzapereka mwayi kwa anthu amene akana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo kuti azitha kugwira ntchito zina. Kuchokera pa nthawi imene dziko la Azerbaijan linalowa m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya padutsa zaka zoposa 13 ndipo dzikoli silinakwaniritsebe zimene linalonjeza.

M’chaka cha 2011 depatimenti ina ya Bungwe la Mayiko a ku Ulaya lomwe limayang’anira zoti anthu asamachite zinthu mwatsankho (ECRI), linatulutsa lipoti lonena za boma la Azerbaijan. Lipotilo linanena kuti: “Dipatimenti ya ECRI ikulimbikitsa akuluakulu a boma la Azerbaijan kuti ayambe kutsatira lamulo limene limapereka ufulu kwa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Mayiko onse amene ali m’bungweli amatsatira lamulo limeneli. . . . . [Dipatimenti ya ECRI] inatsindikanso kuti akuluakulu a bomali asamaimbe milandu kapena kutsekera m’ndende anthu amene akana kulowa usilikali koma aziwapatsa mwayi wogwira ntchito zina zomwe ndi zogwirizana ndi chikumbumtima chawo.”

Anamukakamiza Kulowa Usilikali Komanso Anamutsekera M’ndende Ngakhale kuti Sanalakwe

Boma la Azerbaijan likupitiriza kuphwanya ufulu wa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Mwachitsanzo, pa August 23, 2013 Kamran Shikhaliyev yemwe ndi wa Mboni za Yehova ndipo anali ndi zaka 17 pa nthawiyo, anaitanidwa ku ofesi ina ya boma yolemba asilikali (SSMC) ku Baku Nizani kuti akamuyeze ngati angayenere kulowa usilikali. Kuyambira nthawi imeneyo, Kamran wakhala akufotokozera akuluakulu a ofesiyi kuti sakufuna kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake ndipo wakhala akupempha kuti amupatse ntchito zina. Pa October 8, 2013 Kamran anapereka kalata yake yopempha kuti amupatse ntchito zina m’malo mwa usilikali. Atapita kuti akaonanenso ndi akuluakulu olemba anthu ntchito ya usilikali pa October 10, 2013, akuluakulu a boma la Azerbaijan anamugwira n’kumukakamiza kulowa usilikali. Apolisi anamutenga n’kukamupereka m’manja mwa asilikali ndipo akumusungabe kumalo amene kumakhala asilikali.

Pa April 16, 2014, patadutsa miyezi yoposa 6 kuchokera pamene anamangidwa, Khoti la asilikali la Jalilabad linagamula kuti kwa chaka chimodzi Kamran akhale m’ndende imene amalangilako asilikali. Popereka chigamulochi, khotilo linkaona Kamran ngati ndi msilikali amene akuthawa ntchito yake kapena amene waphwanya malamulo. Koma Kamran sanalumbirepo kuti ndi msilikali, sanavalepo yunifomu ya usilikali kapena kugwira ntchito ya usilikali. Kuwonjezeranso pamenepo nthawi zonse akaitanidwa ku ofesi yolemba asilikali ija sankajomba ndipo pamaulendo onsewa ankafotokoza kuti chikumbumtima chake sichikumulola kugwira ntchito ya usilikali.

Kamran anachita apilo chigamulo chimene anapatsidwa koma pa July 16, 2014, Khoti la apilo la ku Shirvan linakana apiloyo. Panopa Kamran adakali m’manja mwa asilikali ndipo sanamupititsebe ku ndende imene amalangirako asilikali mogwirizana ndi chigamulo chimene anamupatsa. Choncho tingati chigamulo chimene anapatsidwa sichinayambe kugwira ntchito ngakhale kuti wakhala ali m’manja mwa asilikali kuyambira mu October 2013. Kamran akuyembekezera kuti Khoti Lalikulu la m’dziko la Azerbaijan lidzavomera kuti achite apilo mlanduwu komanso lidzavomereza zoti ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake.

Zimene Zakhala Zikuchitika

 1. December 2014

  Kamran Shikhaliyev amusamutsira ku ndende ina ya asilikali ku Salyan m’dziko la Azerbaijan.

 2. September 16, 2014

  Kamran Shikhaliyev akusungidwabe mokakamiza ndi asilikali komanso sanayambe kulandira chilango mogwirizana ndi chigamulo chimene anamupatsa choti akhale m’ndende kwa chaka chimodzi.

 3. April 16, 2014

  Kamran Shikhaliyev anamugamula kuti akhale m’ndende kwa chaka chimodzi chifukwa chokana kugwira ntchito ya usilikali. Ndendeyi ndi kumene amalangilako asilikali.

 4. October 10, 2013

  Ofesi yolemba anthu ntchito ya usilikali inagwira ndi kukakamiza Kamran kuti alowe usilikali ndipo anakamupereka kumene kumakhala asilikali.

 5. March 12, 2013

  Kamran Mirzayev yemwe ndi wa Mboni za Yehova anamupeza kuti ndi wolakwa ndipo anamugamula kuti akhale m’ndende miyezi 9 atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake. Ali kundende, bungwe limene limaona za ufulu wa anthu linamuthandiza ndipo anatuluka m’ndende asanamalize chigamulo chakecho.

 6. September 25, 2012

  Fakhraddin Mirzayev yemwe ndi wa Mboni za Yehova anamupeza kuti ndi wolakwa ndipo anamugamula kuti akhale m’ndende chaka chimodzi atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake.

 7. September 8, 2010

  Farid Mammadov yemwe ndi wa Mboni za Yehova anamupeza kuti ndi wolakwa ndipo anamugamula kuti akhale m’ndende miyezi 9 atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake.

 8. August 19, 2009

  Mushfig Mammedov anamangidwanso atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake, anamutsekera m’ndende pamene ankayembekezera kuti akaonekere kukhoti ndipo anamulipitsa atapezeka kuti ndi wolakwa pa ulendo wachiwiri umene anaimbidwa mlanduwu.

 9. March 7, 2008

  Maloya omwe ankaimira a Mushfig Mammedov ndi a Samir Huseynov anachita apilo ku khoti loona za ufulu wa anthu ku Ulaya kuti boma la Azerbaijan likuzunza anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo.

 10. October 4, 2007

  Samir Huseynov yemwe ndi wa Mboni za Yehova anamugamula kuti akhale m’ndende miyezi 10 atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake.

 11. 2006

  Mushfig Mammedov yemwe ndi wa Mboni za Yehova anamutsekera m’ndende pamene ankayembekezera kuti akaonekere kukhoti. Kenako anamupeza kuti ndi wolakwa atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake ndipo anamulamula kuti azikaonekera ku polisi komanso kuti asapalamule mlandu pa miyezi 6 yotsatira.