Pitani ku nkhani yake

FEBRUARY 18, 2016
AZERBAIJAN

Dziko la Azerbaijan Linapeza Kuti Irina Zakharchenko ndi Valida Jabrayilova Ndi Olakwa Koma Kenako Linawamasula

Dziko la Azerbaijan Linapeza Kuti Irina Zakharchenko ndi Valida Jabrayilova Ndi Olakwa Koma Kenako Linawamasula

Mlandu wa Irina Zakharchenko ndi Valida Jabrayilova unazengedwa kukhoti lina la mumzinda wa Baku pa 28 January 2016. Azimayiwa anapitabe kukhotilo ngakhale kuti anali atatopa ndiponso atafooka. Iwo anatsekeredwa m’kachipinda kazitsulo ngati kuti ndi zigawenga ndipo ankamvetsera pamene woweruza mlanduwo, dzina lake Akram Gahramanov, ankalengeza chigamulo chawo. Woweruzayo anagamula kuti azimayiwo ndi olakwa chifukwa choti ankafalitsa mabuku achipembedzo popanda chilolezo cha boma. Iye analamula kuti apereke chindapusa cha ndalama zokwana madola 4,361 a ku United States. Koma popeza kuti anali atakhala kale m’ndende kwa miyezi 11, woweruzayo ananena kuti asalipire chindapusacho ndipo anawamasula m’ndende.

Anaikidwa M’ndende Popanda Zifukwa Zomveka

Unduna woona zachitetezo wa dziko la Azerbaijan unanena kuti Irina Zakharchenko ndi Valida Jabrayilova, omwe ndi a Mboni za Yehova, anaphwanya malamulo a dzikolo pamene anapatsa mayi wina amene ndi neba wawo kabuku kofotokoza Baibulo mumzinda wa Baku. Undunawu unafufuza nkhaniyi kwa milungu 10 ndipo unapanikiza azimayiwa ndi mafunso. Undunawo unaitana azimayiwa pa 17 February 2015 ndipo atapita anadabwa kuti anthu a mu undunawo anawatenga n’kupita nawo kukhoti kuti akaimbidwe mlandu. * Kenako anaikidwa m’ndende mpaka nthawi imene mlandu wawowu unazengedwa.

Ngakhale kuti mlandu wa a Irina ndi a Valida unali usanazengedwe, akuluakulu a boma anachita zinthu ngati kuti azimayiwo ndi zigawenga zomwe “zikhoza kusokoneza anthu.” Loya wina wa azimayiwo anati: “Ndinadabwa wofufuza mlanduwu atafotokoza mokokomeza kwambiri zimene azimayiwa anachita. Wofufuzayo ananena kuti iwo anachita kupangana kuti aphwanye malamulo mwadala. Koma zoona zake n’zakuti a Valida ankangobwerera kunyumba kwa mayi wina amene poyamba anasangalala atakambirana naye za m’Baibulo ndiponso anali atapempha mabuku achipembedzo. Mayiyo anauza a Valida ndi a Irina kuti alowe m’nyumba mwake kuti akamwe tiyi ndipo analandira kabuku kenakake kachipembedzo kamene azimayiwo anabweretsa.”

Anachitira Nkhanza Azimayiwa Komanso a Mboni Ena Ambiri

Kachipinda kazitsulo kakukhoti

Pa miyezi 11 imene azimayiwa anali m’ndende, akuluakulu a boma anawaika m’chipinda chaokha ndipo sankalola kuti anthu abwere kudzawaona, kulankhula nawo pa foni, kuwalembera makalata kapena kuti akhale ndi Baibulo. Nthawi zonse apolisi ankawavutitsa komanso kuwapanikiza ndi mafunso. Izi zinapangitsa kuti azimayiwa awonde, azisowa tulo ndiponso kuti afooke. Khotilo linakana maapilo ndiponso zimene maloya anapempha zoti litulutse azimayiwo m’ndende n’kungowauza kuti asamachoke pakhomo mpaka mlandu wawo utazengedwa.

Pa nthawi yomvetsera mlanduwu mu May, July ndiponso mu September 2015, unduna woona zachitetezo unapempha khotilo kuti liwonjezere nthawi imene azimayiwo akhale m’ndende. Nthawi yoti mlanduwu uzengedwe itakwana m’mwezi wa December, woweruza Gahramanov anaimitsa mlanduwu katatu. Izi zinachititsa kuti a Irina ndi a Valida akhale m’ndende pafupifupi chaka chathunthu khoti lisanagamule mlandu wawo pa 28 January 2016.

Zimene zinachitika kukhoti zinasonyeza kuti unduna woona zachitetezo unkafuna kugwiranso a Mboni ena. Undunawu unapempha khoti kuti lisungebe azimayiwo m’ndende n’cholinga choti ufufuze a Mboni ena amene unkati ankaphwanyanso malamulo. Pamene azimayiwo anali m’ndende, akuluakulu a boma ankavutitsa a Mboni za Yehova ku Baku. Ankawapanikiza ndi mafunso ndipo pofufuza zinthu ankalowa m’nyumba zawo komanso m’nyumba yawo yolambirira.

Mabungwe ndiponso Anthu Osiyanasiyana Anapempha Boma Kuti Litulutse Azimayiwo

A Mboni za Yehova anapempha kuti mabungwe ena oona za ufulu wa anthu am’mayiko ena athandize a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova kuti atuluke m’ndende. Iwo analemba makalata opita ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya komanso ku nthambi zina za United Nations. A Mboni za Yehova padziko lonse anatumiza makalata ambiri kwa akuluakulu a boma la Azerbaijan. Anthu ena oimira Mboni za Yehova anakapempha thandizo kwa akuluakulu a boma m’mayiko amene akukhala ndiponso anatumiza makalata kwa pulezidenti wa dziko la Azerbaijan opempha kuti athandize azimayiwo.

Pa 2 December 2015, Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka linanena kuti zimene dziko la Azerbaijan likuchitira azimayiwo zikuwaphwanyira ufulu ndiponso zikusonyeza tsankho pa nkhani ya chipembedzo. Gululi linapempha akuluakulu a boma kuti amasule a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova m’ndende n’kuwapatsa chipukutamisozi chifukwa chowasunga m’ndende popanda zifukwa zomveka. Tsiku lotsatira, Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapempha kuti boma la m’dzikoli litulutse a Irina Zakharchenko m’ndende kuti akakhale pa ukaidi wosachoka panyumba chifukwa chakuti ankadwaladwala.

Anagamulidwa Kuti Ndi Olakwa Popanda Zifukwa Zomveka

Pa nthawi yozenga mlanduwu, neba wa a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova uja ananena kuti azimayiwa anamupatsa kabuku. Koma kenako popereka umboni wake mayiyu anafotokoza zinthu zosokoneza ndiponso zosiyana ndi zimene ananena poyamba. Iye sanathe kufotokoza bwino chimene azimayiwo anamulakwira. Kenako woweruza Gahramanov anapereka mwayi kwa a Irina ndi a Valida kuti afunse mayiyo mafunso. Iwo anasonyeza mwaulemu kuti umboni wa mayiyo si woona komanso unkatsutsana. Azimayi awiriwa anauza mayiyu kuti amukhululukira.

Woweruza anamvanso umboni wina kwa anthu ena omwe ananena kuti anaona azimayiwo akufalitsa mabuku achipembedzo popanda chilolezo cha boma. Anthuwa anali atasainira zikalata zonena kuti a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova anaphwanya malamulo koma anavomera kuti anasainira zikalatazo asanaziwerenge. Atafunsidwa, anthuwo anavomeranso kuti sakuwadziwa a Irina ndi a Valida komanso kuti azimayiwa sanawapatsepo mabuku alionse achipembedzo. Woweruzayo anawerenga umboni wa munthu wina wachitatu koma umboni wake unalinso wotsutsana.

Ngakhale kuti umboni unasonyeza kuti a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova sanaphwanye malamulo, woweruza Gahramanov anagamula kuti iwo ndi olakwa. Mlanduwu utatha, loya wina wa azimayiwa anati: “Ndikuona kuti chigamulochi ndi chosamveka ngakhale pang’ono. Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka litaona zimene zikuchitikira azimayiwa, linapempha boma kuti liwatulutse m’ndende ndiponso liwapatse chipukutamisozi. Ngakhale kuti pangopita milungu yochepa kuchokera pamene gululi linapempha zimenezi, woweruza wagamula kuti azimayiwo ndi olakwa.” Panopa azimayiwa akuganiza ngati angachite apilo chigamulo chopanda chilungamochi kapena ayi.

Kodi Dziko la Azerbaijan Lidzasiya Liti Kuchitira Nkhanza Mboni za Yehova?

Panopa gulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova likusangalala kumva kuti a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova anatulutsidwa m’ndende ndipo akusamaliridwa bwino ndi mabanja awo komanso akulandira thandizo la mankhwala. Koma a Mboni akudabwa kwambiri kuti dziko la Azerbaijan linalola bwanji kuti azimayi awiri omwe ndi okonda mtendere komanso osalakwa achitiridwe nkhanza chonchi. Akudabwanso kuti bomali linalola bwanji kuti khoti la m’dzikoli ligamule kuti azimayiwa ndi olakwa popanda zifukwa zomveka.

Anthu ambiri akugwirizana ndi a Mboni podandaula kuti dziko la Azerbaijan laphwanya kwambiri ufulu wachipembedzo wa anthu. Anthu apadziko lonse ali ndi chidwi kuti aone ngati boma la Azerbaijan lingasiye kuchitira nkhanza anthu am’zipembedzo zing’onozing’ono zam’dzikolo. A Mboni za Yehova akuyesetsabe kuti akambirane ndi bomali nkhani zokhudza kulambira kwawo n’cholinga choti amange mfundo imodzi.

^ ndime 4 Pa 10 November 2015, munthu wina wa mu unduna woona zachitetezo anaimba mlandu azimayiwa wophwanya Chigawo 167-2.2.1 cha buku la malamulo a dziko la Azerbaijan. Chigawochi Mchimaletsa kuti gulu lililonse lizifalitsa mabuku achipembedzo popanda chilolezo cha boma.