Pa 8 February, 2017, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Azerbaijan linapeza kuti a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova ndi osalakwa pamlandu womwe ankazengedwa chifukwa chogawira mabuku a chipembedzo popanda chilolezo cha boma. Woweruza milandu wa khotili, dzina lake Hafiz Nasibov, analengeza kuti khotilo silinapeze mlandu uliwonse pa zimene azimayi a Mboniwo anachita ndipo anasintha zimene makhoti aang’ono anagamula zoti azimayiwo anali olakwa.

Pa nthawi imene mlanduwu unkazengedwa, maloya oimira a Zakharchenko ndi a Jabrayilova ananena motsindika kuti boma linaphwanya ufulu wachibadwidwe wa azimayiwo popanda chifukwa chomveka bwino komanso linawachitira nkhanza. Khotilo linapereka mwayi kwa azimayiwo kuti afotokoze mavuto amene anakumana nawo pa miyezi 11 imene anawatsekera m’ndende asanawazenge mlandu komanso mmene zimenezi zinawakhudzira.

Loya woona za ufulu wa anthu a m’mayiko osiyanasiyana dzina lake Jason Wise ananena kuti: “Ndife osangalala kwambiri kuti khotili lathetsa mlanduwu. Aka ndi koyamba kuti khoti lalikulu kwambiri ku Azerbaijan lisinthe chigamulo cha makhoti ang’onoang’ono pankhani zokhudza a Mboni za Yehova. Tikhulupirira kuti nalonso khoti laling’ono la Baku Sabail lilemekeza ufulu wa azimayiwa woti apatsidwe chipepeso.”