Gulu la UN loona za anthu omangidwa popanda zifukwa zomveka likupempha kuti boma la Azerbaijan litulutse m’ndende a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova. Gululi linanena kuti boma la Azerbaijan linamanga anthuwa ngakhale kuti ankachita zinthu pogwiritsa ntchito ufulu wawo wachipembedzo. Zomwe bomali linachita zinasonyeza kuti likudana ndi anthuwa chifukwa cha chipembedzo chawo komanso pozenga mlanduwu silinatsatire dongosolo loyenera. Zimene gululi likuona kuti zinalakwika ndi kutsekera azimayiwa m’ndende mlandu wawowo usanaweruzidwe komanso kuwaimba mlandu chifukwa chochita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chawo.

Boma la Azerbaijan linali litakananso kale kuchita zimene Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inanena kuti atulutse a Irina m’ndende. Pa 7 January 2016, a Irina sanathe kupita kukhoti chifukwa choti ankadwala. Koma funso n’lakuti, kodi mlanduwu ukamapitirizidwa, woweruza mlanduwu Akram Gahramanov, aweruza nkhaniyi mogwirizana ndi malamulo amene mayiko onse amayenera kutsatira?