Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MARCH 7, 2016
AZERBAIJAN

A Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova Achita Apilo Chigamulo cha Khoti

A Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova Achita Apilo Chigamulo cha Khoti

Pa 9 March 2016, Khoti la Apilo la ku Baku lidzamva madandaulo a Irina Zakharchenko ndi Valida Jabrayilova okhudza zomwe boma la Azerbaijan linawachitira powamanga popanda zifukwa zomveka chifukwa chakuti ankafalitsa mabuku achipembedzo. Azimayiwa akufuna kuti boma lichotse mayina awo m’kaundula wa anthu opalamula milandu, libweze ndalama zimene anawononga pa mlanduwu komanso liwapatse chipukutamisozi chifukwa chowaphwanyira ufulu wawo pa nthawi imene anawatsekera m’ndende pafupifupi chaka chathunthu.

Mlanduwu usanayambe kuzengedwa, Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka linali litanena kuti boma la Azerbaijan linaphwanyira ufulu a Zakharchenko ndi a Jabrayilova ndipo ayenera kupatsidwa chipukutamisozi. Koma pa 28 January 2016, khoti loyamba kuzenga mlanduwu linanyalanyaza zimenezi ndipo linagamula kuti azimayiwa ndi olakwa.