Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JULY 14, 2015
AZERBAIJAN

Dziko la Azerbaijan Lipitirizabe Kusunga M’ndende Azimayi Awiri kwa Miyezi Inanso Iwiri

Dziko la Azerbaijan Lipitirizabe Kusunga M’ndende Azimayi Awiri kwa Miyezi Inanso Iwiri

Pa 4 July, 2015, khoti la ku Sabail linagamula kuti a Mboni awiri apitirizebe kukhala m’ndende ndipo linawonjezeranso miyezi ina iwiri. Zimenezi zikutanthauza kuti mayi Irina Zakharchenko ndi mayi Valida Jabrayilova, apitirizabe kukhala m’ndende mpaka pa 17 September, 2015. Apolisi akunena kuti kuwonjezera nthawiyi kuthandiza kuti iwo akonzekere bwino mlanduwu.

Unduna wa zachitetezo unamanga azimayiwa pa 17 February, 2015 pa mlanduwu wokambirana uthenga wa m’Baibulo ndi anthu ena. Panopa undunawu ukupitirizabe kufunsa a Mboni ena zokhudza mlanduwu.