Pitani ku nkhani yake

MAY 19, 2015
AZERBAIJAN

Boma la Azerbaijan Likupiritirizabe Kusunga M’ndende Azimayi Awiri Popanda Mlandu

Boma la Azerbaijan Likupiritirizabe Kusunga M’ndende Azimayi Awiri Popanda Mlandu

Unduna Woona za Chitetezo m’dziko la Azerbaijan wanena kuti a Mboni za Yehova awiri, mayi Irina Zakharchenko ndi mayi Valida Jabrayilova, apitirizebe kukhala m’ndende pamene akuyembekezera kuti mlandu wawo uzengedwe. Pa 17 May, 2015, undunawu unati azimayi awiriwa ali ndi mlandu wogawira mabuku ofotokoza Baibulo “popanda chilolezo” ndipo anawamanga. Pa 7 May, 2015, nalonso khoti la ku Sabail linagwirizana ndi zoti a Mboniwa apitirizebe kukhala m’ndende mpaka pa July 17. Khotili linakana pempho loti azimayi awiriwa azichita ukaidiwo wosachoka panyumba. Maloya omwe akuimira azimayiwa achita apilo chifukwa cha kumangidwa kopanda chilungamo kwa azimayiwa ndiponso akudera nkhawa kuti zimenezi zisokoneza kwambiri thanzi ndi maganizo awo. Apolisi akupitirizabe kufufuza a Mboni ena.