Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

APRIL 12, 2016
AZERBAIJAN

A Polisi ku Azerbaijan Anasokoneza Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu

A Polisi ku Azerbaijan Anasokoneza Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu

Pa 23 March, 2016, apolisi m’dera lina lotchedwa Gakh ku Azerbaijan anafika pa nyumba ina yomwe munali a Mboni za Yehova omwe ankachita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. A Mboni amachita mwambowu chaka chilichonse ndipo amaona kuti ndi wopatulika kwambiri. Apolisiwo anaimitsa mwambowu ndipo anaonetsa zipepala zomwe ankati ndi chilolezo chochokera ku khothi kuti adzachite chipikisheni ndipo analanda mabuku ndi ma Baibulo omwe anthuwo ankagwiritsa ntchito. Kenako anatenga onse amene anasonkhana m’nyumbayi n’kupita nawo kupolisi kumene anawafunsa mafunso komanso kuwalamula kuti aliyense alembe lipoti. Apolisiwo analemba pamodzi malipoti omwe anthu 6 anapereka n’cholinga chakuti akawagwiritse ntchito ngati umboni wosonyeza kuti anthuwa ankaphwanya malamulo kenako anamasula anthu onsewo.