Pa 2 December 2016, ofesi ya apolisi ya ku Goranboy ku Azerbaijan lidasumira mlandu a Ziyad Dadashov atawapeza akulalikira. Anthu 4 omwe amakhala m’mudzi umodzi ndi a Dadashov, anapereka umboni wakuti a Dadashov omwe ndi a Mboni za Yehova amauza anthu zomwe amakhulupirira komanso kugawira mabuku ophunzitsa za Baibulo. Woweruza mlandu m’khoti la ku Goranboy, a Shirzad Huseynov, anapeza kuti a Dadashov ndi olakwa chifukwa chochita zinthu zachipembedzo * zomwe akuti n’kuphwanya malamulo ndipo anawauza kuti alipire ndalama zokwana 1, 500 manat (omwe ndi madola 846 a ku United States). Koma a Dadashov akuona kuti si zomveka kuti apatsidwe chilangochi ndipo akukonza zochita apilo chigamulocho.

M’boma lomweli, a Jaarey Suleymanova ndi a Gulnaz Israfilova anapita kunyumba ya mayi wina yemwe akhala akukambirana naye nkhani za m’Baibulo kwa miyezi yambiri. Ali kunyumbako, kunabwera apolisi ndipo anawagwira chifukwa chowapeza akukambirana nkhani zachipembedzo zomwe amati n’zosemphana ndi malamulo. Pa 17 November, 2016 woweruza milandu m’khoti la ku Goranboy a Ismayil Abdurahmanli, analipiritsa azimayi awiriwa ndalama zokwana 2,000 manat (omwe ndi madola 1,128 a ku United States). Azimayiwa akukonza zochita apilo nkhaniyi.

Loya woona za ufulu wa anthu m’mayiko osiyanasiyana a Jason Wise, ananena kuti: “Zimene boma la Azerbaijan likuchita pozunza a Mboni za Yehova, zikusonyeza kuti bomali silikutsatira zomwe mayiko anagwirizana m’pangano lokhudza ufulu la mayiko a ku Europe. Komanso akuluakulu a boma ku Goranboy, akuchitanso zinthu zosemphana ndi zomwe malamulo a dzikolo amanena. Malamulo a dziko la Azerbaijan amalola anthu kuchita zinthu mogwirizana ndi zomwe amakhulupirira kuchipembedzo chawo.”

^ ndime 1 A Mboni za Yehova analembetsa chipembedzo chawo m’kaundula wa boma ku Baku lomwe ndi likulu la dziko la Azerbaijan. A Dadashov anaweruzidwa potengera zimene gawo 515.0.4 lokhudzana ndi milandu imanena. Komatu gawoli limanena za “chipembedzo chosavomerezeka mwa malamulo.”