Pitani ku nkhani yake

Zokhudzana ndi Malamulo Komanso Ufulu Wachibadwidwe

 

AZERBAIJAN

Dziko la Azerbaijan Linapeza Kuti Irina Zakharchenko ndi Valida Jabrayilova Ndi Olakwa Koma Kenako Linawamasula

N’chifukwa chiyani azimayi awiri osalakwa omwe akhala akuchitiridwa nkhanza ndi boma anagamulidwa kuti ndi olakwa?

SOUTH KOREA

Komiti ina ya United Nations Yapempha Dziko la South Korea Kuti Lipereke kwa Anthu Ufulu Wokana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Mayiko ambiri ali ndi chidwi kuti aone ngati boma la South Korea litsatire zimene komiti ya UN yapempha n’kuchita zinthu mogwirizana ndi Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale.

RUSSIA

Khoti la Taganrog Linapereka Chilango kwa a Mboni Chifukwa Chochita Zachipembedzo

A Mboni onse 16 anapezeka kuti ndi olakwa pa mlandu wochita zinthu zoopsa zobweretsa chisokonezo. Chigamulochi chikhoza kuchititsa kuti a Mboni am’madera ambiri ku Russia aziimbidwa mlandu chifukwa chochita zachipembedzo.

RUSSIA

Khoti la ku Taganrog Lagamula kuti a Mboni za Yehova 16 Ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zachipembedzo

Chigamulochi chingachititse kuti a Mboni apitirize kuzunzidwa ndiponso kumangidwa chifukwa cha chipembedzo chawo ku Russia.

SOUTH KOREA

A Mboni a ku Korea Anapereka Madandaulo Awo ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka

Mayiko ena komanso makhoti a m’dziko la South Korea akufuna kuti dzikolo lisiye kumanga anthu amene amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, m’malo mwake liziwapatsa mwayi wogwira ntchito zina.

TURKMENISTAN

Dziko la Turkmenistan Linagamula Kuti a Bahram Hemdemov Akhale M’ndende Zaka 4 Chifukwa cha Chipembedzo

Apolisi anaphwanya malamulo posokoneza msonkhano umene unkachitikira m’nyumba ya a Bahram Hemdemov. Akuluakulu a makhoti anachitanso zinthu mopanda chilungamo.

SOUTH KOREA

Khoti Lalikulu ku South Korea Lipereka Chigamulo pa Nkhani ya Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Khotili linaimitsa mlanduwu kuti liganize kaye ngati malamulo a asilikali onena kuti anthu okana usilikali ayenera kulandira chilango akugwirizana ndi malamulo a dziko kapena ayi.

RUSSIA

Zimene Mneneri wa Mboni za Yehova Ananena Zokhudza Mlandu wa ku Taganrog, M’dziko la Russia

Kuyambira mu 2011, a Mboni 16 akhala akuimbidwa mlandu chifukwa chochita zachipembedzo chawo. Kodi n’zoona kuti ali ndi mlandu wochita zinthu zoopsa zimene zingabweretse chisokonezo?

UKRAINE

Khoti Lalikulu ku Ukrain Lagamula Kuti Anthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali pa Zifukwa za Chipembedzo

Khoti lalikulu lagwirizana ndi zimene makhoti ang’onoang’ono anagamula zoti munthu ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali ngakhale pa nthawi yomwe m’dziko muli ziwawa za ndale kapena nkhondo.