Pitani ku nkhani yake

Zokhudzana ndi Malamulo Komanso Ufulu Wachibadwidwe

 

SOUTH KOREA

A Mboni za Yehova Omwe Ali M’ndende ku South Korea Aperekanso Madandaulo Ena

Dziko la South Korea likupitiriza kuzunza anyamata omwe ndi a Mboni za Yehova powaika m’ndende chifukwa chogwiritsa ntchito ufulu umene ali nawo wopembedza komanso wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

BULGARIA

Bungwe Loona Zamalamulo ku Bulgaria Ladzudzula Mchitidwe wa Tsankho Limene Limachitika Chifukwa Chosiyana Zipembedzo

Siteshoni ya TV ya SKAT ku Bulgaria komanso atolankhani ake awiri awalamula kuti alipire chindapusa chachikulu kwambiri chifukwa chowulutsa nkhani zimene zinayambitsa zipolowe komanso kuchititsa kuti anthu azidana ndi a Mboni za Yehova.

RWANDA

Boma la Rwanda Lathetsa Tsankho Limene Limachitika M’masukulu Chifukwa cha Kusiyana kwa Zipembedzo

Zimene boma lachita poteteza ufulu wopembedza umene ana a sukulu ali nawo ndi nkhani yosangalatsa kwambiri kwa ana a sukulu omwe ndi a Mboni.

TURKEY

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula kuti Dziko la Turkey Liyenera Kuvomereza Nyumba za Ufumu Monga “Malo Olambirira”

Ngakhale kuti zinthu zakhala zikuyenda bwino kwa a Mboni za Yehova pankhani zamalamulo, iwo akuvutikabe chifukwa malamulo a dziko la Turkey sakuwalola kumanga komanso kukhala ndi malo olambirira ovomerezeka.

SOUTH KOREA

Kodi Dziko la South Korea Liyamba Kulemekeza Ufulu wa Anthu Wochita Zinthu Mogwirizana ndi Zimene Amakhulupirira?

A Seon-hyeok Kim, omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo sagwira ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, poyamba anawapeza kuti ndi wosalakwa pa mlandu woti ankazemba usilikali. N’chifukwa chiyani khoti la apilo linasintha chigamulochi n’kunena kuti a Kim ndi wolakwa?

RUSSIA

Zimene Dziko la Russia Likuchita Pofuna Kutseka Likulu la Mboni za Yehova Zikusokoneza Ufulu Wawo Wolambira Mulungu Momasuka

A Mboni m’dziko la Russia akhoza kukhala ndi ufulu wokhulupirira zimene akufuna koma osakhala ndi ufulu wochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo.

DERA LA PALESTINA

A Mboni za Yehova Akuvutika Kuti Apatsidwe Ufulu Wonse Kudera la Mapalestina

Si bwino kuti a Mboni azichitiridwa tsankho posaloledwa kulembetsa chipembedzo chawo m’kaundula zomwe zikuchititsa kuti asamalandire ufulu wawo wonse.

KYRGYZSTAN

Kodi Apolisi Amene Anachitira Nkhanza a Mboni a ku Osh Adzapatsidwa Chilango?

A Mboni za Yehova akupempha ofesi ya loya wamkulu wa boma kuti achitepo kanthu ndipo apereke chilango kwa apolisi amene anachita nkhanzawo.