Pitani ku nkhani yake

Zokhudzana ndi Malamulo Komanso Ufulu Wachibadwidwe

 

RUSSIA

Apolisi Ayamba Kuchitira Nkhanza a Mboni za Yehova ku Russia

Popeza kuti akuluakulu a boma la Russia anatseka mabungwe oimira Mboni za Yehova, tsopano ayamba kuukira munthu aliyense yemwe ndi wa Mboni komanso chilichonse chimene angachite chokhudza kulambira.

ERITREA

A Mboni za Yehova Awiri Achikulire Anafera M’ndende ku Eritrea

A Habtemichael Tesfamariam ndi a Habtemichael Mekonen anafera m’ndende ya Mai Serwa chakumayambiriro kwa chaka cha 2018. A Mboniwa anamangidwa ndi kuikidwa m’ndende mopanda chilungamo chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo anakhala mozunzika m’ndendemo kwa zaka pafupifupi 10.

KAZAKHSTAN

A Teymur Akhmedov Anakhululukidwa ndi Pulezidenti Ndipo Anatulutsidwa M’ndende

Pulezidenti wa ku Kazakhstan Nursultan Nazarbayev anakhululukira a Teymur Akhmedov omwe ndi a Mboni za Yehova, atakhala m’ndende kwa chaka ndi miyezi chifukwa chouzako ena zimene amakhulupirira. Zimenezi zachititsa kuti asakhalenso ndi mbiri yoti anapalamulapo mlandu m’dzikolo.

TURKMENISTAN

Dziko la Turkmenistan Likukana Kupereka Ufulu Wotsatira Zimene Munthu Amakhulupirira

A Mboni awiri anaweruzidwa kuti akakhale m’ndende chifukwa chokana usilikali. Dziko la Turkmenistan likukanabe kupereka ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira ndipo sililola kuti anthu azigwira ntchito ina m’malo mwa usilikali.

SOUTH KOREA

A Mboni ku South Korea Anapempha Pulezidenti kuti Athetse Kumanga Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

A Mboni akudikira pamene akuluakulu a boma akuganizira nkhani yokhudza kumanga anthu amene akana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

SOUTH KOREA

Makhoti a ku South Korea Akufufuza Njira Yabwino Yochitira Zinthu ndi Anthu Okana Usilikali

Oweruza a ku South Korea akufufuza njira yothandizira anthu okana usilikali m’malo mongowamanga. Khoti loona za malamulo lipereka chigamulo pa nkhaniyi.

ARMENIA

Boma la Armenia Lazindikira Kuti Anthu Okana Usilikali Ali Ndi Ufulu

Zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe lakhala likugamula, zathandiza kwambiri dziko la Armenia pa nkhani yopereka ntchito zina kwa anthu okana usilikali ndipo panopa zinthu zikuyenda bwino.

RUSSIA

Akuluakulu a boma la Russia Alanda Nyumba ya Misonkhano ya Mboni za Yehova

Patadutsa wiki imodzi kuchokera pamene khoti linapereka chigamulo choopseza kuti litenga maofesi a Mboni n’kuwasandutsa likulu la dziko la Russia, akuluakulu a boma analanda Nyumba ya Misonkhano. Nyumbayi ili pafupi ndi St. Petersburg.