Moto wolusa womwe unayamba pa 23 July, 2018, ukupitiriza kuyaka pafupi ndi mzinda wa Redding ku California. Motowu, womwe ukudziwika ndi dzina la komwe unayambira, wapha anthu 8, wawononga malo opitirira maekala 110,000, komanso wawononga nyumba zopitirira 1,300.

Panopa sitinalandire lipoti losonyeza kuti pali wofalitsa amene wavulala kwambiri ndi motowu, komabe m’bale wathu wina anapsa pang’ono pamene ankayendetsa chinamatcheni pofuna kuthandiza ozimitsa moto. Kuonjezera pamenepa, abale ndi alongo 454 anathawa m’nyumba zawo ndipo akukhala m’nyumba za achibale awo kapena za ofalitsa ena mongoyembekezera. Komanso nyumba za mabanja 12 a Mboni zinaonongeka ndi motowu.

Palibe wofalitsa aliyense amene akusowa ndipo oyang’anira madera limodzi ndi akulu a m’derali akuyesetsa kuthandiza ofalitsawa powalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo komanso kuwapatsa zinthu zofunikira pa nthawi yovutayi.—Miyambo 17:17.