Pitani ku nkhani yake

MAY 31, 2019
UNITED STATES

Zokhudza Misonkhano ya Mayiko ya 2019 Yakuti “Chikondi Sichitha”

Zokhudza Misonkhano ya Mayiko ya 2019 Yakuti “Chikondi Sichitha”

Miami, Florida (Chisipanishi), United States

  • Masiku: 24 mpaka 26 May, 2019

  • Malo: Marlins Park ku Miami, Florida, United States

  • Chinenero: Chisipanishi

  • Chiwerengero cha Osonkhana: 28,562

  • Chiwerengero cha Obatizidwa: 230

  • Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 4,600

  • Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Bolivia, Brazil, Britain, Canada, Central America, Central Europe, Chile, Colombia, Cuba, Ecuador, Paraguay, Peru, Philippines, ndi Spain

Abale ndi alongo a ku Florida akulandira alendo omwe abwera ku Miami

Ana a Mboni atatu akujambulitsa chithunzi pafelemu panja pa malo omwe kunachitikira msonkhanowu

M’bale Kenneth Cook wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka

Anthu 4 akubatizidwa

Abale ndi alongo akuimba nyimbo pa nthawi ya msonkhano pa tsiku Loweruka

Mlongo wa ku Florida ali limodzi ndi mlendo ndipo akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri panja pa Kislak Center, ku koleji ya Miami Dade

Abale ndi alongo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera aima m’bwalo la malo amsonkhano pa nthawi ya nkhani yomaliza pa tsiku Lamlungu

Alongo akukonzekera kugawa zakudya zotchedwa chorizo, empanadas, komanso paella pa nthawi yochereza alendo

Alongo a ku Florida akuvina gule wachikhalidwe cha ku Spain pa nthawi yomwe anthu anakumana pamodzi madzulo

Alendo ochokera kumayiko ena akusangalala ndi zochitika zosiyanasiyana ku malo a msonkhano ku West Palm Beach