Pitani ku nkhani yake

Komwe kunachitikira chiwembuchi, kumaofesi oyang’anira mzinda wa Virginia Beach

JUNE 4, 2019
UNITED STATES

Anthu Ambiri Aomberedwa ku Virginia Beach M’dziko la United States

Anthu Ambiri Aomberedwa ku Virginia Beach M’dziko la United States

Pa 31 May, 2019, munthu wina yemwe anali ndi mfuti anaombera anthu ogwira ntchito kumaofesi oyang’anira mzinda wa Virginia Beach womwe uli ku Virginia m’dziko la United States. Anthu okwana 12 anaphedwa komanso ena 4 anavulala.

Ofesi ya nthambi ya ku United States yanena kuti n’zomvetsa chisoni kuti mlongo LaQuita Brown ndi mmodzi wa anthu omwe anaphedwa pa chiwembuchi. Mlongo Brown anali ndi zaka 39 ndipo anali mpainiya wokhazikika mumpingo wa Chifulenchi wotchedwa Seaview womwe uli mumzinda wa Norfolk ku Virginia. Iye ankatumikiranso m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga. Akulu komanso woyang’anira dera akulimbikitsa anzake a Mlongo Brown ndiponso achibale ake pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

Tikumva chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya mlongo wathuyu. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zinthu zoipa ngati zimenezi sizidzachitikanso ndipo padziko lapansi padzakhala “mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.