Pitani ku nkhani yake

FEBRUARY 9, 2018
TAIWAN

Ku Taiwan Kunachitika Chivomezi Champhamvu

Ku Taiwan Kunachitika Chivomezi Champhamvu

Lachiwiri pa 6 February usiku, m’madera omwe ali kum’mawa kwa Taiwan pafupi ndi m’mbali mwa nyanja munachitika chivomezi champhamvu. Ofalitsa nkhani ananena kuti anthu 6 anafa komanso ena oposa 250 anavulala. Anthu enanso 76 sakudziwika kumene ali.

Palibe wa Mboni aliyense amene anafa kapena kuvulala ndi chivomezichi. Komabe chivomezichi chinawononga nyumba imene muli maofesi a omasulira m’chinenero cha anthu a ku Taiwan chotchedwa Amis komanso Nyumba ya Ufumu. Nyumbazi zili mu mzinda wa Hualien, ndipo n’kumene chivomezichi chinawononga kwambiri. Komanso nyumba imene omasulira ena ankakhala inawonongeka kwambiri moti sangakhalemonso. Zimenezi zitachitika, nthawi yomweyo a Mboni a m’derali anakonza malo ongoyembekezera oti a Mboni anzawo amene anakhudzidwa ndi chivomezichi akhalemo. Nayonso ofesi ya nthambi ya ku Taiwan ikuyesetsa kupereka zofunikira zina.

Tikupemphera kuti Yehova athandize abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi kuti akhale ndi mtendere wam’maganizo pa nthawi yovutayi. Komanso kuti abale omwe ali ndi udindo wowasamalira kuti akhaledi “ngati malo obisalirapo mphepo.”—Yesaya 32:2.

Media Contacts:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Taiwan: Chen Yongdian, +886-3-477-7999