Pitani ku nkhani yake

SEPTEMBER 18, 2019
SOUTH KOREA

Akhristu a ku South Korea Anakana Kulowa Usilikali—Nkhani Yosonyeza Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima Kwawo

Akhristu a ku South Korea Anakana Kulowa Usilikali—Nkhani Yosonyeza Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima Kwawo

Kuyambira mu 1953, abale achinyamata a ku Korea akhala akumangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Tikaphatikiza zaka zonse zimene abale athu oposa 19,000 akhala ali m’ndende, zikukwana 36,000. Koma pa 28 February 2019, m’bale womalizira amene anali adakali m’ndende, anatulutsidwa. Kodi zinthu zosaiwalikazi zinatheka bwanji? Tiyeni tione mmene abale athu a ku Korea anasonyezera chikhulupiriro komanso kulimba mtima.