NEW YORK—Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linatumiza abale ochokera m’mayiko osiyanasiyana kupita ku Moscow ngati njira imodzi yosonyezera kuti a Mboni za Yehova padziko lonse ali limodzi ndi abale ndi alongo awo ku Russia pa nthawi yovutayi.

Abalewa atafika ku Russia analandiridwa ndi abale ndi alongo a m’dzikolo omwe ankaoneka osangalala kwambiri. Ena mwa abale ndi alongowa anali ochokera m’madera akutali kwambiri monga ku Siberia. A Mboni ochokera m’mayiko enawo anatsimikizira abale awo a ku Russia kuti abale ndi alongo awo padziko lonse akuwadera nkhawa komanso kupitirizabe kuwapempherera. M’modzi wa abale amene anapita nawo ku Russia anati: “Zinandikhudza kwambiri nditaona kulimba mtima kwa abale ndi alongo anga a ku Russia. Iwo sanafooke, makamaka tikaganiziranso kuti panalibiretu chiyembekezo chilichonse kuti khotili lingasinthe chigamulo chopanda chilungamo chimene linapereka poyamba.”

Ngakhale kuti oweruza atatu anagamula mopanda chilungamo, abale ndi alongo ku khotiko ankachita kuonekeratu kuti amakondana komanso kuti ndi ogwirizana. Zinali zomvetsa chisoni kwambiri kuona dzina la Yehova likunyozedwa poyera kumalo ngati amenewa komanso kudziwa kuti abale ndi alongo athu ku Russia apitiriza kukumana ndi mayesero aakulu kwambiri. Komabe chikondi komanso ulemu umene abale anasonyeza m’khotimo zinali umboni woti milandu yachinyengo yomwe akuwaimba mlandu kuti ndi kagulu koopsa ndi yosamveka. Zinalinso umboni wosonyeza kuti oweruzawo sanagamule nkhaniyi mwachilungamo.

A Mark Sanderson, omwe ndi a m’Bungwe Lolamulira ndi amene anatsogolera abale ochokera m’mayiko enawa ku Russia. M’bale Sanderson analimbikitsa abale a ku Russia kuti alimbe mtima komanso kuti asaope zilizonse zimene angakumane nazo. Pomwe abale a m’mayiko enawa ankachoka kukhotiko, abale a ku Russia anawakumbatira komanso kuwathokoza chifukwa chodzakhala nawo pa nthawi yapaderayi.

Kenaka abale ochokera m’mayiko enawa anapita kumaofesi a akazembe a mayiko 21 mumzinda wa Moscow kuti akafotokoze zinthu zankhanza zimene boma la Russia likuchitira a Mboni za Yehova. Zina mwa nkhanzazi ndi monga kuwaotchera nyumba, kuwachotsa ntchito komanso kuopseza ana awo akapita kusukulu. Akulu ambiri kuphatikizapo m’bale Dennis Christensen akuimbidwa mlandu wotsogolera misonkhano yophunzira Mawu a Mulungu yomwe boma la Russia likuti ndi yosaloledwa. Padakali pano m’bale Christensen akumusungabe m’ndende ngakhale kuti mlandu wake sunazengedwe. Akazembe angapo anakhudzidwa kwambiri ndi kavidiyo kamene anawaonetsa, kosonyeza nkhanza zimene boma la Russia likuchita. Ambiri mwa ogwira kumaofesi a akazembewa ankafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova akuwachitira zinthu ngati zimenezi?” Abale athu anapezerapo mwayi wofotokoza kuti a Mboni za Yehova salowerera ndale komanso kuti ntchito yathu yolalikira yathandiza kwambiri kusintha moyo wa anthu ambiri ku Russia. Kazembe wina ananena kuti: “A tchalitchi cha Orthodox amadana nanu chifukwa amaona kuti mumawatengera anthu awo.” Pa nthawi imene mlandu wa a Mboni unkazengedwa, maofesi a akazembe 10 anatumiza nthumwi zawo ku khotiko ndipo nthumwizo zinakhala nawo kukhotiko tsiku lonse.

Pamene abale ochokera m’mayiko osiyanasiyanawa ankachoka ku Russia, n’kuti chikhulupiriro chawo chitalimba kwambiri komanso atakhudzidwa chifukwa choona kukhulupirika kwa abale awo ku Russia. Chikhulupiriro chawo chinalimbanso chifukwa cha mwayi umene anali nawo wolalikira kwa akuluakulu a kumaofesi a akazembe.

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000