Pitani ku nkhani yake

Khoti la mumzinda wa Oryol

MAY 14, 2019
RUSSIA

Posachedwapa Khoti Limaliza Kumvetsera Dandaulo la a Christensen

Posachedwapa Khoti Limaliza Kumvetsera Dandaulo la a Christensen

Lachiwiri pa 7 May, 2019, khoti la mumzinda wa Oryol linayamba kumvetsera dandaulo la a Dennis Christensen lokhudza chigamulo choti akakhale m’ndende kwa zaka 6 chifukwa chochita zinthu zokhudza zimene amakhulupirira. Pofika pano, khotili lakana kuganizira bwinobwino mfundo zimene maloya a a Christensen akuona kuti ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti a Christensen ndi osalakwa, ndipo n’zimenenso makhoti ena a m’dziko la Russia akhala akuchita. Oweruza atatu omwe akuzenga mlanduwu mwina akhoza kupereka chigamulo chawo pofika kumapeto kwa mlungu uno.

Pa tsiku loyamba lomwe khoti linkamvetsera dandauloli, abale ndi alongo ambiri anapita kukhotiko kuti akalimbikitse m’bale Christensen. Kunabweranso nthumwi zochokera m’mayiko osiyanasiyana, atolankhani, komanso omenyera ufulu wa anthu. Kumvetsera mlanduwu kunayambira m’kachipinda kakang’ono komwe kanali kokwana anthu 20 kapena 25 okha, ndipo izi zinachititsa kuti anthu pafupifupi 50 akanizidwe kulowa. Komabe, maloya oimira a Christensen pamlanduwu anapempha kuti asamukire m’chipinda chokulirapo chomwe mukanakwana anthu pafupifupi 80, ndipo khoti linavomereza pempholi. Khoti linaimitsa kaye kumvetsera mlanduwu patangotha maola atatu okha.

Pa tsiku lachiwiri lomvetsera mlanduwu, oweruza anakana pempho la maloya a a Christensen lakuti khotilo liunikenso maumboni ambiri omwe analipo osonyeza kuti a Christensen ndi osalakwa. Komatu zimenezi n’zomvetsa chisoni, chifukwa maloyawa anali ndi chikhulupiriro chakuti maumboniwo asonyezanso kuti a Christensen anamangidwa pa zifukwa zopanda umboni. Pamapeto pake, khotilo linalengeza kuti lidzapitiriza kumvetsera mlanduwu lachinayi pa 16 May, pamene adzamvetsere komaliza kuchokera ku mbali zonse zokhudzidwa.

Tikupitiriza kupempherera abale athu ku Russia kuti asasiye kukhala mwamtendere komanso kudalira kwambiri lonjezo la Yehova loti adzawateteza kwa aliyense wowanyodola.—Salimo 12:5.