Pitani ku nkhani yake

M’bale Valeriy Moskalenko ali mu selo pa nthawi ya mlandu wake

AUGUST 30, 2019
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lipereka Chigamulo pa Mlandu wa M’bale Moskalenko Mlungu Wamawa

Khoti la ku Russia Lipereka Chigamulo pa Mlandu wa M’bale Moskalenko Mlungu Wamawa

Woweruza milandu dzina lake Ivan Belykh wa khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy ku Khabarovsk, wanena kuti apereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Valeriy Moskalenko azaka 52, pa 2 September, 2019.

M’bale Moskalenko wakhala ali m’ndende kuchokera pa 2 August, 2018, pamene oimira gulu lina la zachitetezo (FSB) komanso apolisi oletsa chipolowe anathyola n’kulowa m’nyumba mwawo. Anthuwa anafufuza m’nyumba mwa M’baleyu kwa maola 5 ndipo kenako anamumanga. Popeza kuti a Moskalenko akhala ali m’ndende koposa chaka poyembekezera kuwazenga mlandu, pali nkhawa yoti mwina akhoza kugamulidwa kuti akhalebe m’ndende ngati mmene zinakhalira ndi a Dennis Christensen.

Pa 18 December, 2018, a Mboni anakadandaula za mlandu wa a Moskalenko v. Russia ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Palinso milandu ina yoposa 50 yomwe inatumizidwa kukhotili yokhudza boma la Russia. Pa milandu imeneyi, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe launikapo kale milandu 34.

Timawanyadira abale ndi alongo athu okondedwa a ku Russia ‘chifukwa cha kupirira kwawo ndi chikhulupiriro chawo pokumana ndi mazunzo ndi masautso onse amene akulimbana nawo.’ Zikuchita kuonekeratu kuti Yehova akuwathandiza komanso kuwadalitsa. Tikupempha Yehova kuti apitirize kupereka mphamvu kwa M’bale Moskalenko kuti athe kupirira, mosatengera chigamulo chomwe akapatsidwe mlungu wamawa.—2 Atesalonika 1:4.