Pitani ku nkhani yake

M’bale ndi Mlongo Akopyan (kutsogolo pakati) komanso anthu ena omwe anapita kukhoti kukakhala nawo.

MARCH 6, 2019
RUSSIA

Khoti Lasintha Chigamulo cha M’bale Akopyan ku Russia

Khoti Lasintha Chigamulo cha M’bale Akopyan ku Russia

Pa 1 March, 2019, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Republic of Kabardino-Balkaria linasintha chigamulo chomwe khoti laling’ono linapanga choti M’bale Arkadya Akopyan ndi wolakwa. Iwo anakhala akuimbidwa mlandu kwa nthawi yopitirira chaka chimodzi powanamizira kuti ankagawira mabuku “oopsa” komanso ‘ankalimbikitsa anthu kudana ndi anthu azipembedzo zina.’

Khoti laling’ono linagamula kuti M’bale Akopyan yemwe ali ndi zaka 70 apatsidwe chilango choti agwire ntchito yothandiza m’dera lawo. Chigamulo chomwe Khoti Lalikulu Kwambiri lapanga posachedwapa chinasintha chigamulo cha khoti laling’onolo.

Tikuyamikira Yehova chifukwa cha chigamulo chosangalatsachi ndipo tikusangalala ndi M’bale Akopyan. Tipitiriza kupemphera kuti abale athu apitirize kupirira mokhulupirika.—2 Atesalonika 1:4.