Pitani ku nkhani yake

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: A Aleksey Budenchuk, a Konstantin Bazhenov, a Feliks Makhammadiyev, a Aleksey Miretskiy, a Roman Gridasov, ndi a Gennadiy German, asanamangidwe

SEPTEMBER 23, 2019
RUSSIA

Abale Enanso 6 ku Russia Awapeza Olakwa Ndipo Awatsekera M’ndende

Abale Enanso 6 ku Russia Awapeza Olakwa Ndipo Awatsekera M’ndende

Lachinayi pa 19 September, 2019, abale 6 ochokera mumzinda wa Saratov ku Russia anawapeza olakwa ndipo anawatsekera m’ndende chifukwa choti ndi a Mboni za Yehova.

Woweruza wa khoti la m’boma la Leninsky mumzinda wa Saratov dzina lake Dmitry Larin, anagamula kuti M’bale Konstantin Bazhenov ndi M’bale Aleksey Budenchuk akhale m’ndende kwa zaka zitatu ndi miyezi 6. M’bale Feliks Makhammadiyev anagamulidwa zaka zitatu pomwe M’bale Roman Gridasov, M’bale Gennadiy German, komanso M’bale Aleksey Miretskiy anagamulidwa zaka ziwiri. Kuwonjezera pamenepa, abale onsewa anauzidwanso kuti akadzamaliza kugwira ukaidi wawo, sadzaloledwa kupatsidwa udindo wotsogolera bungwe lililonse la boma kwa zaka 5. Abalewa akufuna kupanga apilo chigamulochi.

Abale 6 amenewa anawatsegulira milandu pambuyo pa chipikisheni chomwe apolisi a ku Russia anachita m’nyumba 7 za a Mboni ku Saratov pa 12 June, 2018. Abale onsewa ali ndi mabanja ndipo M’bale Budenchuk ali ndi ana awiri omwe adakali pasukulu. Atamangidwa, M’bale Budenchuk, M’bale Bazhenov komanso M’bale Makhammadiyev anakhala m’ndende pafupifupi chaka chimodzi milandu yawo isanazengedwe.

Polankhula komaliza m’khoti, abalewa anagwira mawu a m’mavesi ambiri a m’Baibulo omwe anawalimbikitsa kukhalabe okhulupirika ndiponso ananena kuti sakudana ndi anthu omwe anakawasumira mlandu.

Panopa dziko la Russia lapeza olakwa ndi kutsekera m’ndende azibambo 7. Abale ndi alongo oposa 250 anawapeza ndi milandu ku Russia, ndipo 41 anawatsekera m’ndende (poyembekezera kuwazenga mlandu kapena atawapeza olakwa), pomwe 23 ali pa ukaidi wosachoka panyumba.

Tikupempherera abale ndi alongo athu onse okhulupirika komanso olimba mtima a ku Russia ‘kuti alandire mphamvu zazikulu chifukwa cha mphamvu [za Yehova] zaulemerero, kuti athe kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.’—Akolose 1:11.