Pitani ku nkhani yake

Khoti la mumzinda wa Oryol

MAY 17, 2019
RUSSIA

A Dennis Christensen Akapempha Komaliza Kuti Khoti Lisinthe Chigamulo pa 23 May

A Dennis Christensen Akapempha Komaliza Kuti Khoti Lisinthe Chigamulo pa 23 May

Lachinayi pa 16 May, 2019, khoti linapitiriza kumvetsera mlandu wa apilo wa a Dennis Christensen mogwirizana ndi zimene khotilo linanena. Patsikuli, oimira boma pa milandu komanso maloya a a Christensen analankhula mawu awo omaliza, ndipo a Christensen analankhula pafupifupi ola limodzi podziteteza. Nthumwi zochokera m’mayiko osiyanasiyana komanso atolankhani anabweranso patsikuli, zomwe zikusonyeza kuti ngakhale kuti patha zaka ziwiri kuchokera pamene nkhani yokhudza kumangidwa kwa a Christensen inafalitsidwa m’mayiko osiyanasiyana, anthu padziko lonse adakali ndi chidwi ndi mlandu wa a Christensen.

Poyamba, kumvetsera mlanduwu kumayenera kutha Lachisanu pa 17 May. Komabe, oweruza milandu analengeza kuti aimitsa kaye mlanduwu mpaka Lachinayi pa 23 May nthawi ya 10:00 m’mawa. Patsikuli, a Christensen adzapatsidwa mwayi womaliza woyankhula m’khoti, oweruza milandu asapereke chigamulo chawo. N’zovuta kudziwa ngati khotili lidzalengeza chigamulo chake pa 23 May kapena ngati lidzalengeza chigamulocho tsiku lina m’tsogolo.

Timalimba mtima tikaona abale athu monga a Dennis Christensen komanso a Sergey Skrynnikov akupitiriza kukhala ndi maganizo abwino komanso kusonyeza mochokera pansi pamtima kuti ndi ofunitsitsa kukhalabe okhulupirika. Tikamaganizira za a Mboni anzathu ku Russia, timamva mofanana ndi mmene mtumwi Paulo anamvera chifukwa cha kupirira kwa abale a ku Tesalonika. Mouziridwa, iye analemba kuti: “Ifeyo timakunyadirani ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pokumana ndi mazunzo ndi masautso onse amene mukulimbana nawo.”—2 Atesalonika 1:4.