Pitani ku nkhani yake

Nyumba za abale athu zomwe zinapsa ndi moto ku Taguig City, Metro Manila

MAY 21, 2019
PHILIPPINES

Moto Wawotcha Nyumba za Anthu ku Philippines

Moto Wawotcha Nyumba za Anthu ku Philippines

Mu March 2019, moto unawotcha nyumba 128 mumzinda wa Calbayog pachilumba cha Samar ku Philippines. M’mwezi wa February 2019, moto unabuka mumzinda wa Taguig womwe uli pachilumba cha Luzon. Nyumba zonse za a Mboni za Yehova zomwe zinapsa ndi motowu zinakwana 7. Abale ndi alongo athu omwe anathawa m’nyumba zawo chifukwa cha motowu panopa akukhala ndi a Mboni ena omwe sanakhudzidwe ndi ngoziyi.

Ofesi ya nthambi inathandiza mwamsanga poyendetsa ntchito yopereka chakudya, madzi komanso zovala. Akulu a m’mipingo ya m’maderawa analimbikitsa abale okhudzidwa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso anapereka chithandizo. Makomiti Othandiza Pangozi Zadzidzidzi awiri mothandizidwa ndi abale a m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga akukonzekera ntchito yomanganso nyumba za abale athuwa.

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kukhala pothawirapo pa abale omwe akhudzidwa ndi motowu.—Salimo 62:8.