Pa 24 October, 2018, mphepo yamphamvu kwambiri yotchedwa Yutu inawononga kwambiri ku zilumba zakumpoto kwa Mariana. Zilumba zikuluzikulu za Saipan ndi Tinian ndi zimene zinakhudzidwa kwambiri ndi mphepo yomwe inkathamanga pamtunda wa makilomita 280 pa ola, imene inawononga nyumba komanso inachititsa kuti magetsi azime m’nyumba za anthu ambiri.

Ofesi ya nthambi ya Micronesia yomwe imayang’anira ntchito za a Mboni ku zilumba za kumpoto kwa Mariana, inanena kuti palibe wa Mboni amene anaphedwa kapena kuvulala ndi mphepoyi. Komabe, nyumba 15 za a Mboni zinawonongekeratu ndipo zina 40 zinawonongeka. Kuwonjezera pamenepo, nyumba ya amishonale ku Saipan komanso Nyumba za Ufumu ku Saipan ndi ku Tinian zinawonongeka pang’ono.

Komiti Yopereka Chithandizo Pangozi Zadzidzidzi ikuyendetsa ntchito yopereka zinthu zofunika kwa anthu okhudzidwa. Komanso ofalitsa omwe nyumba zawo zinawonongeka akusungidwa ndi a Mboni anzawo. M’bale wa m’Komiti ya Nthambi apita kumadera omwe anakhudzidwa ndi mphepoyi kuti akalimbikitse abale athu ndi mfundo za m’Baibulo.

Tikupempherera abale athuwa pamene akuyesetsa kupirira mavutowa. Ndipo timatonthozedwa podziwa kuti “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye” komanso “adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Salimo 145:18, 19.