Ntchito yayikulu yomanganso zinthu zomwe zinaonongeka ndi zivomezi idzayamba pa 1 December ndipo ndi ya ndalama pafupifupi madola 10 miliyoni. Ntchitoyi iphatikizapo kumanganso nyumba za anthu pafupifupi 500, Nyumba za Ufumu 16, komanso kukonza zinthu zina zambiri zomwe zaonongeka ndi zivomezi ziwiri zomwe zinachitika mu September ku Guatemala ndi ku Mexico.

MEXICO CITY—Pa 1 December, 2017, Komiti ya Nthambi ku Central America iyambitsa ntchito yayikulu yomanganso zinthu zomwe zinaonongeka ndi zivomezi ziwiri zomwe zinachitika mu September, ku Guatemala ndi ku Mexico. Zivomezi zitangochitika, ofesi ya nthambi ya Central America inathandiza abale omwe anakhudzidwa ndi zinthu monga madzi, chakudya, mankhwala, komanso zovala. Gawo lachiwiri lothandiza anthu omwe anakhudzidwa likhala kumanganso Nyumba za Msonkhano, Nyumba za Ufumu, komanso nyumba za abale.

Abale ndi alongo okwana 655 a m’madera a Chiapas ndi Oaxaca ku Mexico, anathawa m’nyumba zawo chifukwa cha chivomezi champhamvu kwambiri chomwe chinachitika pa 7 September. Ntchito yothandiza anthu a m’madera awiriwa ikuphatikizapo kumanganso nyumba za anthu zokwana 315 ndi Nyumba za Ufumu 15. Kuonjezera pamenepo, akuyembekezeranso kukonza nyumba za anthu zokwana 1,039, Nyumba za Ufumu 108, komanso Nyumba za Msonkhano 3.

Chivomezi champhamvu chomwe chinachitika pa 19 September mu mzinda wa Mexico City ndi m’maboma a Mexico, Morelos, ndi Puebla, chinachititsa kuti abale ndi alongo okwana 463 asowe malo okhala. Nyumba zokwana 158 zimangidwanso, komanso akufunika kukonza nyumba za anthu 600, Nyumba za Ufumu 39, ndi Nyumba ya Msonkhano imodzi.

Chivomezi chomwe chinachitika pa 7 September ku Guatemala, chinachititsa kuti abale ndi alongo 36 asowe malo okhala. M’miyezi ikubwerayi, abale ogwira ntchito zomangamanga komanso ongodzipereka amanga nyumba za anthu zokwana 9 ndi Nyumba ya Ufumu imodzi. Agwiranso ntchito yokonza nyumba 20 ndi Nyumba za Ufumu 4.

Abale a m’Komiti ya Nthambi akuganiza kuti ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwawa, yomwe igwiridwe ndi makomiti 39 othandiza pangozi zadzidzidzi, ikhala ya ndalama pafupifupi madola 10 miliyoni ndipo itenga miyezi 5 kapena 6. Abale ogwira ntchito zomangamanga okwana 30 akukonza zosamukira m’madera amene akhudzidwa, ndipo anthu enanso 970 adzipereka kuti athandiza pa ntchito yomanganso zinthu zomwe zinaonongeka. Tikukhulupirira kuti Yehova adalitsa ntchitoyi komanso mtima wodzipereka wa onse amene akuchita “nawo utumiki wothandiza” abale athu omwe akhudzidwa ndi zivomezizi.—2 Akorinto 8:4.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Guatemala: Juan Carlos Rodas +502-5967-6015

Mexico: Gamaliel Camarillo, +52-555-133-3048