MEXICO CITY—Pa 4 December 2017, gulu la anthu m’katauni ka Tuxpan de Bolaños, komwe kali kumapiri a m’dera la Jalisco ku Mexico, linaukira abale athu 12 amtundu wa Huichol komanso anthu ena 36 omwe amagwirizana nawo ndipo anawathamangitsa m’nyumba zawo. Gululi linakwiya chifukwa choti a Mboni sankachita nawo miyambo ina ya chipembedzo cha anthu amtunduwu. Abale athu anakadandaula za nkhaniyi kwa akuluakulu a boma.

Katundu wa abale athu anabedwa kapena kutayidwa kunja.

Akuluakulu a boma amalemekeza miyamboyi komanso chikhalidwe cha mtunduwu moti amawapatsa ufulu wambiri. Atsogoleri a anthu amtunduwu ndi amene anauza gululo kuti lithamangitse abale m’nyumba zawo ndipo linaba zitseko, mawindo komanso malata. Zinthu zina zonse zimene gululi silinatenge linazitaya kunja. Kenako gululi linapita ndi abalewo kutchire n’kuwauza kuti akangobwerera kwawoko liwapha.

Abale amtundu wa Huichol ali panja pa Nyumba ya Ufumu.

Abale ochokera ku ofesi ya nthambi ku Mexico anapita kukalimbikitsa abalewo komanso kukaona zimene angachite kuti awapezere pokhala. Maloya oimira Mboni za Yehova anapita kukakambirana ndi akuluakulu a boma oyang’anira zamalamulo komanso ufulu wa anthu. Panopa akuluakulu abomawo akufufuza za nkhaniyi.

M’bale Gamaliel Camarillo amene amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Mexico ananena kuti: “Tikudabwa kuti Akhristu anzathu amene amakhala mwamtendere komanso amalemekeza miyambo ya anthu ena akuzunzidwa chifukwa choti sanachite nawo miyambo imene sigwirizana ndi zimene amakhulupirira. Sitikukayikira kuti akuluakulu a boma athandiza mwamsanga anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chipembedzo chawowa.”

Tikupempherera abale athu omwe panopa alibe nyumba komanso katundu wawo watengedwa ndipo sitikukayikira kuti Yehova agwiritsa ntchito gulu lake powathandiza.—Yes. 32:2.

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Mexico: Gamaliel Camarillo, +52-555-133-3048