Zinthu zikuyambiranso kuyenda bwino ku Madagascar pambuyo pa mphepo yamkuntho ya Ava, yomwe inaomba m’dzikoli pa 5 January, 2018. Akuluakulu a boma alengeza kuti anthu pafupifupi 51 amwalira ndipo ena ambiri akusowa pokhala.

Ngoziyi itangochitika, ofesi ya nthambi ya ku Madagascar inafufuza ndipo inapeza kuti palibe wa Mboni aliyense amene wamwalira. Komabe nyumba za anthu zokwana 45 komanso Nyumba za Ufumu zokwana 6 zinaonongedwa ndi mphepoyi. Kuonjezera pamenepa, mphepoyi inaononganso mbewu zomwe zimathandiza ofalitsa ambiri kupeza zakudya ndi zinthu zina pamoyo wawo. Zimenezi zitangochitika, ofesi ya nthambi inakhazikitsa komiti yothandiza anthu pakachitika ngozi zadzidzidzi. Komitiyi inapereka zinthu zofunikira kwa ofalitsa omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi monga zakudya, zovala ndi kuwamangira nyumba zongoyembekezeramo. Abale awiri ochokera ku ofesi ya nthambi anapita kumadera omwe mphepoyi inaomba ndipo anapangitsa msonkhano wapadera ndi mabanja onse amene anakhudzidwa pofuna kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Malemba.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi limene limayendetsa ntchito yopereka thandizo kwa anthu okhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi kuphatikizapo ngozi yomwe yachitika ku Madagascar. Iwo amagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo zothandizira ntchito ya Mboni yomwe ikuchitika padziko lonse. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kukhala malo a chitetezo kwa abale ndi alongo athu a ku Madagascar pa nthawi yovutayi.—Salimo 9:9, 10

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Madagascar: Rinera Rakotomalala, +261-33-37-012-91