Lachiwiri pa 4 September, 2018, m’madera akumadzulo kwa Japan munachitika mphepo yamkuntho yoopsa kwambiri. Ndipo malipoti akusonyeza kuti mphepoyi ndi yamphamvu kwambiri kuposa mphepo zina zimene zinaombapo m’dzikoli zaka zoposa 20 zapitazo. Akuluakulu a m’maderawa anauza anthu onse kuti achoke m’nyumba zawo ndipo mogwirizana ndi zimene ankayembekezera, mphepoyi inawononga zinthu zambiri.

Ofesi ya nthambi ku Japan yatsimikizira kuti palibe wa Mboni za Yehova aliyense amene wafa chifukwa cha mphepoyi. Komabe, abale ndi alongo osachepera 15 anavulala ndipo nyumba zosachepera 538 zinaonongeka. Kafukufuku yemwe anachitika koyamba akusonyezanso kuti Nyumba za Ufumu 44 zinaonongeka.

Makomiti othandiza pakachitika ngozi zadzidzidzi a ku Osaka ndi ku Sakai akugwira ntchito mogwirizana pokonzekera kuthandiza anthu okhudzidwa komanso kukonza nyumba zoonongeka ndi kupanga maulendo aubusa.

Tikuthokoza kuti Yehova amadziwa mavuto onse amene Akhristu anzathu akukumana nawo ndipo akuwathandiza pogwiritsa ntchito ubale wapadziko lonse.—Salimo 34:19.