Pitani ku nkhani yake

SEPTEMBER 17, 2019
JAPAN

Mphepo Yamphamvu Kwambiri ya Faxai Yawomba ku Japan

Mphepo Yamphamvu Kwambiri ya Faxai Yawomba ku Japan

Pa 9 September, 2019, mphepo yamphamvu kwambiri yotchedwa Faxai inaomba pafupi ndi mzinda wa Tokyo ku Japan. Mphepoyi inkathamanga pamtunda wamakilomita 180 pa ola ndipo inachititsa kuti nyumba 580,000 zikhale zopanda magetsi. Anthu osachepera atatu anaphedwa.

Ofesi ya nthambi ku Japan yanena kuti palibe wofalitsa yemwe anaphedwa koma abale ndi alongo 7 anavulala. Malipoti oyambirira akusonyeza kuti mphepoyi inawononga nyumba 895 za abale athu, Nyumba za Ufumu 28, komanso Malo a Msonkhano amodzi a mumzinda wa Chiba.

Ofesi ya nthambi ikupitiriza kufufuza mmene mphepo ya Faxai yakhudzira abale athu. Tikupemphera kuti Yehova, “Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza,” apitirize kuthandiza abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.—Aroma 15:5.