Pitani ku nkhani yake

SEPTEMBER 10, 2019
JAPAN

Madzi Asefukira ku Japan

Madzi Asefukira ku Japan

Pa 28 August, 2019, mvula yamphamvu yomwe inagwa m’chigawo cha Kyushu ku Japan inachititsa kuti madzi asefukire kwambiri. Mitsinje inasefukira ndiponso panali chiopsezo choti nthaka ikanatha kugumuka m’madera ena, zomwe zinachititsa kuti anthu oposa 800,000 auzidwe kuti achoke m’nyumba zawo. Ofesi ya nthambi ku Japan yanena kuti ofalitsa 82 anathawa m’nyumba zawo. Malinga ndi malipoti aposachedwapa, nyumba 40 za abale athu zinawonongeka ndiponso Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka pang’ono.

Ofesi ya nthambi yakhazikitsa Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi kuti ithandize ofalitsa omwe akhudzidwa. Oyang’anira madera, limodzi ndi akulu komanso ofalitsa, akutonthoza ndiponso kulimbikitsa abale athu omwe akhudzidwa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso kuwapatsa zinthu zofunika monga chakudya ndi zovala. Tikuyamikira kwambiri kuti chikondi chikuchititsa abale ndi alongo ambiri kuthandiza abale athu omwe akhudzidwa ndi madzi osefukirawa.—2 Akorinto 8:4.