Pitani ku nkhani yake

SEPTEMBER 26, 2019
ITALY

Ku Italy Kunachitika Mwambo Wokumbukira a Mboni za Yehova Omwe Anazunzidwa ndi Chipani cha Nazi

Ku Italy Kunachitika Mwambo Wokumbukira a Mboni za Yehova Omwe Anazunzidwa ndi Chipani cha Nazi

Chikwangwani chomwe chinaikidwa m’nyumba yotchedwa Risiera di San Sabba, mumzinda wa Trieste. A Mboni za Yehova omwe anaikidwa m’ndende yozunzirako anthu ankavala mayunifomu okhala ndi chizindikiro cha kansalu kapepo

Pa 10 May, 2019, akuluakulu a boma, akatswiri olemba mbiri, atolankhani, komanso alendo ambirimbiri anapezeka pamwambo wotsegulira chikwangwani chokumbukira abale ndi alongo athu masauzande omwe anazunzidwa ndi a chipani cha Nazi komanso ndi anthu omwe ankatsatira boma la Italy pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Mwambowu unachitikira m’nyumba yotchedwa Risiera di San Sabba yomwe ili mumzinda wa Trieste, kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Italy. Poyamba, nyumbayi inali chigayo cha mpunga ndipo pambuyo pake inadzakhala ndende yokhayo yozunzirako anthu komwe mitembo ya akaidi omwe aphedwa inkaotchedwako. Atolankhani osiyanasiyana a m’dzikoli anabwera kumwambowu kuphatikizapo atolankhani a TV yotchedwa Canale 5, yomwe ndi imodzi mwa ma TV omwe anthu ambiri m’dzikoli amaonera.

Potsegulira mwambowu, a Christian Di Blasio omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Italy, anakamba nkhani yomwe inatsindika za kukhala okhulupirika. Iwo anati: “Ndi a Mboni za Yehova okha omwe anazunzidwa ndi ulamuliro wa chipani cha Nazi chifukwa cha zimene ankakhulupirira. Iwo analinso gulu lokhalo lomwe linali ndi mwayi wosankha kuti asazunzidwe. Ankangofunika kunena kuti asiya kutsatira zomwe amakhulupirira monga Akhristu ndipo ayamba kuchita zofuna za boma. Koma ngakhale anali ndi mwayi wochita zimenezi, iwo analimba mtima n’kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu komanso kusonyeza chikondi kwa ena.” Kenako M’bale Di Blasio anaonetsa vidiyo yosonyeza Mlongo Emma Bauer akufotokoza mmene iyeyo ndi banja lake anazunzidwira pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Mlongoyu anafotokoza kuti Akhristu oona sasiya zomwe amakhulupirira ngakhale atauzidwa kuti aphedwa. Pamapeto pa mwambowu, meya wa mzinda wa Trieste, a Roberto Dipiazza, nawonso anayankhula. Iwo anati: “Ndine wosangalala chifukwa cha chikwangwanichi. Tiyenera kuchitapo kanthu kuti nkhanza ngati zimenezi zisadzachitikenso.” Kenako anachotsa nsalu yomwe anavindikira pa chikwangwanicho.

Akatswiri amaphunziro ndi anthu ena otchuka ambiri analankhula za kufunika kwa mwambowu. Mwachitsanzo, pulezidenti wakale wa bungwe lina la chipembedzo (Federation of Evangelical Churches in Italy) dzina lake Giorgio Bouchard, anati: “Kupatula a Mboni za Yehova, palibe chipembedzo china chomwe anthu ake ambiri anaphedwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. . . . Ngakhale kuti a Mboni anazunzidwa kwambiri, nkhanza zomwe anachitidwa zinawathandiza kuti akhale olimba. A Mboni za Yehova anasonyeza kwa anthu, ndipo tikukhulupirira kuti anasonyezanso kwa Mulungu, kuti anali chipembedzo chokhacho chomwe sichinkagwirizana ndi mfundo za boma la Nazi.” (Kuti mudziwe zambiri, onani bokosi m’munsimu.)

Pali chiyembekezo choti chaka chilichonse anthu pafupifupi 120,000 azipita kukaona chikwangwanichi ku Risiera di San Sabba. Mlendo aliyense adzakhala ndi mwayi woona chikwangwanichi pokumbukira a Mboni za Yehova ambirimbiri omwe anakhalabe okhulupirika pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse ngakhale kuti ankazunzidwa ndi chipani cha Nazi komanso boma la Italy.—Chivumbulutso 2:10.