Pitani ku nkhani yake

MAY 31, 2019
ISRAEL

Ntchito Yolalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri Inawonjezeka ku Israel Alendo Atakhamukira ku Tel Aviv

Ntchito Yolalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri Inawonjezeka ku Israel Alendo Atakhamukira ku Tel Aviv

Kuyambira pa 10 mpaka 19 May, a Mboni za Yehova ku Israel anayesetsa kugwira mwakhama ntchito yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri mumzinda wa Tel Aviv. Iwo anachita zimenezi chifukwa cha kuchuluka kwa alendo omwe anapita kukakhala nawo pa zochitika zosiyanasiyana zokhudza chikhalidwe zomwe zinachitikira mumzindawu. Mwachitsanzo, kuyambira pa 14 mpaka 18 May, alendo pafupifupi 10,000 anakhamukira ku Tel Aviv kumpikisano wa zoimbaimba wotchedwa Eurovision Song Contest.

M’bale Gennadi Korobov yemwe anathandiza nawo kuyendetsa ntchito yolalikirayi anati: “Titadziwa kuti kumpikisano wa zoimbaimba wa ku Tel Aviv kudzapezeka alendo masauzande ambiri, tinaona kuti umenewu ndi mwayi waukulu woti tiwonjezere ntchito yathu yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Tinasangalala kwambiri kuti ofalitsa 168 ochokera m’mipingo 22 ya ku Israel anadzipereka kugwira nawo ntchito yolalikirayi.”

Tsiku lililonse abale ankaika timashelefu tamabuku m’malo 8 osiyanasiyana kuyambira 9:00 m’mawa mpaka 9:00 madzulo. Pofuna kuthandiza alendo ochokera m’mayiko osiyanasiyana, timashelefuto tinali ndi mabuku a zinenero 10. Zinenerozi ndi Chiarabu, Chitchainizi, Chingelezi, Chifulenchi, Chijeremani, Chiheberi, Chitaliyana, Chijapanizi, Chirasha, komanso Chisipanishi.

Tikukhulupirira kuti pakhala zotsatira zabwino chifukwa cha kuonjezeka kwa ntchito yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri komwe kunachitika ku Israel. Khama limene abale athuwa anachita ndi umboni wowonjezereka wosonyeza kuti anthu a Yehova amamutamanda “nthawi zonse.”—Salimo 34:1, 2.