Pitani ku nkhani yake

MARCH 28, 2019
INDONESIA

Madzi Asefukira ku Indonesia

Madzi Asefukira ku Indonesia

Pa 16 March, 2019, mvula yamphamvu inagwa chakum’mawa kwa chigawo cha Papua m’dziko la Indonesia. Mvulayi inachititsa kuti madzi asefukire mwadzidzidzi ndipo anapha anthu oposa 100 komanso kuononga nyumba zambiri.

Ofesi ya nthambi ya ku Indonesia yanena kuti abale athu ambiri omwe amakhala m’tawuni ya Sentani m’chigawo cha Papua, akhudzidwa ndi madzi osefukirawa. N’zomvetsa chisoni kuti m’bale wathu m’modzi anafa nyumba yake itakokoloka ndi madzi osefukirawo. Nyumba zinanso zitatu za mabanja a a Mboni zinaonongeka kwambiri. Ofalitsa oposa 40 anasamutsidwa ndipo ambiri tsopano akukhala m’nyumba za a Mboni ena. Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi yakhazikitsidwa kuti iyendetse ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa. Abale ochokera ku ofesi ya nthambi komanso woyang’anira dera, anakayendera kumadera omwe akhudzidwa kukatonthoza ndi kulimbikitsa abale ndi alongo ndi mfundo za m’Baibulo. Iwo akufufuzanso zinthu zomwe abalewa angafunikire komanso kuchuluka kwake.

Tikupempherera abale onse omwe akhudzidwa ndi ngoziyi. Tikuyembekezera mwachidwi tsiku limene Yehova “adzameza imfa kwamuyaya” komanso pamene “adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”—Yesaya 25:8.