Lamlungu pa 3 June, 2018, ku Guatemala kunaphulika chiphala chamoto chapansi panthaka chotchedwa Volcan de Fuego chomwe chinapanga mtsinje komanso chimtambo cha utsi chomwe chinakwera m’mwamba pafupifupi makilomita 9. M’dera lomwe chiphalachi chinaphulika muli mipingo yosachepera 10. Mwamwayi palibe m’bale kapena mlongo yemwe anavulala ngakhale kuti abale ndi alongo 8 anasamutsidwa n’cholinga chofuna kupewa ngozi. Mogwirizana ndi zimene lemba la 2 Akorinto 8:14, 15 limanena, abale a m’madera oyandikana ndi kumene kunaphulika chiphalachi, anapereka malo ogona, zinthu zofunikira komanso thiransipoti.