Kuyambira pa 26 September, 2018, mpaka pa 6 January, 2019, ku malo osungirako mbiri yokhudza nkhanza zomwe zinkachitika mu ulamuliro wa chipani cha Nazi (Munich Documentation Centre for the History of National Socialism) kunachitika chionetsero chapadera. Cholinga chake chinali kufuna kuthandiza anthu kudziwa zomwe a Mboni za Yehova anakumana nazo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi. Malowa ali pamene kale panali likulu la chipani cha Nazi.

Polandira alendo pamwambo wotsegulira chionetserochi, Dr. Hans-Georg Küppers omwe ndi mlangizi pa nkhani za chikhalidwe mumzinda wa Munich, anafotokoza chifukwa chomwe chinawapangitsa kukonza chionetserochi. Iwo anati: “Chionetserochi ndi chofunika chifukwa kwa nthawi yayitali anthu sankaganiza kuti a Mboni za Yehova anazunzidwa mu ulamuliro wa chipani cha Nazi. . . . Cholinga cha chionetserochi n’kuthandiza anthu kudziwa zoona zokhudza a Mboni omwe anazunzidwa.”

Mbiri yofotokoza zomwe abale athu anakumana nazo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi inasonyezedwa pa mabolodi okwana 60 omwe anali ndi nkhani zokhudza kulimba mtima, kukhulupirika, komanso kukhalabe ndi moyo pa nthawi yovuta. Bolodi lina linali ndi nkhani yofotokoza zomwe zinachitikira Martin ndi Gertrud Pötzinger, omwe anamangidwa n’kuwatumiza kundende zozunzirako anthu zosiyana patangotha miyezi yochepa atakwatirana. Zimenezi zinachititsa kuti asaonane kwa zaka 9. Onse anapulumuka ndipo kenako M’bale Pötzinger anadzakhala mmodzi wa abale a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.

A Therese Kühner anaphedwa ndi chipani cha Nazi pa 6 October, 1944.

Bolodi lina linali ndi nkhani yofotokoza za a Therese Kühner, omwe anakhala a Mboni za Yehova (omwe pa nthawiyo ankadziwika kuti Ophunzira Baibulo) mu 1929. A Mboni ataletsedwa ku Germany, misonkhano yachinsinsi ya mpingo inkachitikira m’nyumba mwa a Therese komanso mayiwa anayamba kusindikiza mabuku a Mboni mobisa. A chipani cha Nazi atadziwa zimene mayiwa ankachita, anawamanga powaganizira kuti anapalamula mlandu “wofalitsa ndiponso kugawira mabuku omwe anali otsutsana ndi boma komanso ofooketsa asilikali.” Mlongo Kühner sanasiye kukhala wokhulupirika ngakhale kuti ankadziwa kuti akhoza kuphedwa. Iwo anaphedwa pa 6 October, 1944.

Mabolodi ena ankafotokoza nkhani za abale athu omwe sanachite nawo zandale ndipo anakana kuchitira Hitler sawatcha, zomwe zinachititsa kuti boma la chipani cha Nazi lizidana nawo kwambiri.

Mu 1934, Hitler analumbira kuti athetseratu Mboni za Yehova, ndipo analengeza kuti: “Gulu limeneli litha kuno ku Germany.” A Mboni anapirira pomwe ankazunzidwa kwambiri pamene Hitler ankafuna kukwaniritsa cholinga chake cha nkhanza chimenechi. Panopa Hitler ndi chipani chake kulibeko, pomwe abale athu ku Germany tsopano alipo oposa 165,000. Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa pamene tikukumana ndi mavuto, iye amatipatsa chiyembekezo chomwe “sichitikhumudwitsa.”—Aroma 5:3-5.