Pa 14 ndi 15 October, 2018, mvula yamphamvu kwambiri inagwa m’chigawo cha kum’mwera kwa dziko la France ndipo zimenezi zinachititsa kuti madzi asefukire kwambiri n’kupha anthu osachepera 10.

Lipoti lochokera ku ofesi ya nthambi ya dziko la France linanena kuti abale ndi alongo onse omwe amakhala m’chigawochi ndi otetezeka ngakhale kuti mabanja ena anasamutsidwa chifukwa cha madzi osefukirawa. Katundu wa a Mboni ambiri anawonongeka komanso nyumba zitatu zinaonongeka kwambiri. Dipatimenti Yopereka Chithandizo Pakagwa Tsoka ya ku ofesi ya nthambi yakhala ikupereka chithandizo kwa abale ndi alongo athu.

Tili ndi chikhulupiriro kuti dzanja lamphamvu lamanja la Mulungu ‘liwagwira mwamphamvu’ abale athu amene akupitirizabe kumudalira pa nthawi yovuta kwambiri imeneyi.—Salimo 63:8.