Pitani ku nkhani yake

MARCH 13, 2019
ETHIOPIA

Mlongo Wafa pa Ngozi ya Ndege ku Ethiopia

Mlongo Wafa pa Ngozi ya Ndege ku Ethiopia

Lamlungu pa 10 March, ndege ya ku Ethiopia nambala yake 302 inagwa itangonyamuka kumene ku Addis Ababa, lomwe ndi likulu la dziko la Ethiopia. Mu ndegeyi munali anthu 157 ndipo onse anafa.

N’zomvetsa chisoni kuti mlongo wathu dzina lake Rosemary Mumbi, ndi mmodzi mwa anthu omwe anafa pa ngoziyo. Mlongo Mumbi anali ndi zaka 66 komanso anali mtumiki wa nthawi zonse mumpingo wa Roma Manzoni Inglese ku Rome m’dziko la Italy.

Tili ndi chisoni kwambiri chifukwa cha imfa imeneyi. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene akufa adzaukitsidwa, pamene tidzalandira atumiki okhulupirika a Yehova, kuphatikizapo Mlongo Mumbi.—Chivumbulutso 20:13.