Kuyambira pa 10 mpaka 11 February 2018, mphepo yamkuntho yotchedwa Gita inayamba pang’onopang’ono koma kenako inakula kwambiri n’kufika powononga zinthu ku Samoa ndi American Samoa. Pa 12 February mphepoyi inaombanso ku Tonga ndipo inachititsa kuti madzi asefukire m’derali ndipo zinthu zambiri zinaonongeka.

Palibe wa Mboni aliyense amene anafa kapena kuvulala kwambiri ndi mphepoyi. Komabe nyumba zambiri zinaonongeka kwambiri. Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi anayesetsa kuthandiza anthu okhudzidwa powapatsa zakudya ndi malona.

Ku SAMOA nyumba zokwana 10 zinaonongeka kwambiri.

Ku AMERICAN SAMOA nyumba zitatu zinaonongeka ndi madzi. Abale ndi alongo a m’derali akuyesetsa kupezera anthu amene akusowa pokhala malo oyembekezera oti akhalepo.

Pomwe ku TONGA nyumba 6 zinaonongeka kwambiri. Abale ndi alongo omwe anasoweratu pokhala amakagona mu Nyumba ya Ufumu.

Ndife osangalala kuti palibe m’bale wathu ngakhale mmodzi amene anavulala kwambiri pangoziyi ndipo ambiri omwe anakhudzidwa akuthandizidwa ndi abale awo auzimu. Umenewu ndi umboni wa chikondi chimene Yesu ananena kuti chiyenera kukhala ndi otsatira ake.—Yohane 13:34, 35.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

American Samoa: Panapa Lui, +1-684-770-0064

Samoa: Sio Taua, +685-20629

Tonga: Palu Kanongata’a, +676-25736