Pitani ku nkhani yake

JANUARY 24, 2018
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Kenneth Cook Asankhidwa Kukhala Mmodzi wa Abale a M’Bungwe Lolamulira

A Kenneth Cook Asankhidwa Kukhala Mmodzi wa Abale a M’Bungwe Lolamulira

Lachitatu m’mawa pa 24 January, 2018, ku Beteli ya United States ndi Canada, kunaperekedwa chilengezo choti M’bale Kenneth Cook wasankhidwa kukhala mmodzi wa abale a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. M’baleyu asanaikidwe pa udindowu, anali Wothandiza Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku.

M’bale Kenneth Cook anayamba upainiya pa 1 September, 1982. Ndipo anayamba kutumikira ku nthambi ya ku United States pa 12 October, 1984. Panopa abale onse a m’Bungwe Lolamulira akwana 8.

Tikupempha Yehova kuti apitirize kudalitsa abale a m’Bungwe Lolamulira pamene akutsogolera ntchito za Mboni za Yehova padziko lonse.—1 Atesalonika 5:12, 13

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000