Lachiwiri pa 21 March, 2017, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linapempha a Mboni za Yehova padziko lonse kuti alembe makalata opempha akuluakulu a boma la Russia kuti asinthe maganizo awo ofuna kuletsa ntchito ya a Mboni m’dzikolo. Sizikudziwika kuti ndi makalata angati omwe akuluakulu a boma la Russia analandira, koma anthu ambiri omwe analemba makalatawo analandira makalata ochokera ku boma otsimikiza kuti akuluakulu a bomawo analandira makalata awo. Ngakhale kuti boma la Russia linasankha kugwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika posamvera pempho loti lisaletse ntchito ya a Mboni, kampeni yolemba makalatayi inasonyeza mgwirizano wochititsa chidwi womwe uli m’gulu la Yehova padziko lonse. Kampeniyi inaperekanso umboni kwa abale athu ku Russia woti gulu lonse la abale ndi lokonzeka kuwathandiza.—1 Peter 2:17.

Kamtsikana kakupanga nawo kampeni yolemba makalata ku Bolivia.

A Mboni ambiri anachita khama kuti achite nawo kampeniyi. M’mayiko ena, kutumiza kalata ku Russia kunali kodula kwambiri, choncho amene anali ndi ndalama zokwanira anapereka mowolowa manja n’cholinga choti amene sakanakwanitsa athe kutumiza nawo makalata. Ofalitsa ena anatumiza makalata awo kudzera kwa anzawo omwe amakhala m’mayiko amene kutumiza zinthu n’kotchipa. Abale ndi alongo ambiri ankakumana malo amodzi monga mabanja kapenanso mipingo kuti alembe makalata pamodzi n’kutumiza ambiri pamtengo wotsika. Kuchita zimenezi sikuti kunangothandiza ofalitsawo kupulumutsa ndalama zina basi, koma kunawathandizanso kukhala ogwirizana ndipo zimenezi zinachititsa kuti kampeni yolemba makalatayi ikhale yosaiwalika.

Palinso malipoti osonyeza kuti ogwira ntchito kumalo otumizira makalata ndi katundu anathandiza pa kampeniyi. Mwachitsanzo, bwana woyang’anira ntchito yotumiza katundu mu mzinda wa Barranquilla ku Colombia anati: “Ndinachita chidwi kwambiri ndi mgwirizano umene muli nawo padziko lonse, komanso kuti mukuchita zinthu limodzi pa nkhani ya ku Russia. Ndikukhulupirira kuti zimene zikuchitika kuno ku Barranquilla zikuchitikanso mu mzinda uliwonse padziko lonse. Uthenga umenewu ukhala wamphamvu padziko lonse ndipo ndikukhulupirira kuti anthu enanso aona kuti uthengawu ndi ofunika.” Mu mzinda wa Anseong ku South Korea, woyang’anira malo otumizira makalata anakonza windo lapadera n’cholinga choti a Mboni azitumizirapo makalata, komanso ankapatsa abale ma envelopu mwaulere otumizira makalata ku mayiko akunja.

Abale ndi alongo ku Guinea akumana pamodzi kuti alembe makalata.

A Yaroslav Sivulskiy, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova anafotokoza kuti: “Abale ku Russia atamva kuti Bungwe Lolamulira lakhazikitsa kampeni yolemba makalata padziko lonse m’malo mwawo, anazindikira kuti mulimonse mmene nkhaniyo ingagamulidwire, sikuti anali okha m’chikhulupiriro.”

A Mark Sanderson a m’Bungwe Lolamulira anati: “Kampeni yolemba makalatayi inasonyeza umboni wamphamvu woti anthu a Yehova ndi ogwirizana. Pamene tili kumapeto kwenikweni kwa dzikoli, kukhala ogwirizana ndi kofunika kwambiri kuti tidzathe kupulumuka. Pamene tikuyembekezera kuona zimene Yehova achite ndi nkhani ya ku Russia, tichita chilichonse chomwe tingathe kuti tithandize abale athu. Tipitirizanso kupemphera kwa Yehova mogwirizana, ndipo tili ndi chikhulupiriro kuti Mulungu wathu asamalira abale athu m’njira zosiyanasiyana.”—Salimo 65:2.