Pitani ku nkhani yake

Mmene Mphepo Yamkuntho ya Idai inaonongera kunja kwa mzinda wa Beira m’dziko la Mozambique

MARCH 27, 2019
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mphepo Yamkuntho ya Idai Yaononga Kum’mwera Chakum’mawa kwa Africa

Mphepo Yamkuntho ya Idai Yaononga Kum’mwera Chakum’mawa kwa Africa

Lachinayi pa 14 March, 2019, Mphepo Yamkuntho ya Idai inaononga zinthu ku Mozambique ndipo inapitiriza kuononga ku Malawi ndi ku Zimbabwe. Zikuoneka kuti mphepoyi ndi imodzi mwa mphepo zamphamvu kwambiri pa mphepo zomwe zakhala zikuomba m’chigawo chakum’mwera kwa dziko lapansi ndipo yaononga misewu, nyumba, ndipo anthu oposa 2.6 miliyoni akhudzidwa ndi mphepoyi. Anthu oposa 200 afa kale ndi mphepoyi. N’zomvetsa chisoni kuti mwa anthu omwe afawo, awiri ndi alongo ndipo awiri ndi ana osabatizidwa a ku Mozambique. Ku Zimbabwe, m’bale wazaka 14 anafa nyumba yake itakokoloka ndi matope.

Nyumba ya Ufumu ya Inhamízua yomwe inaonongeka kwambiri ku Mozambique ndi Mphepo Yamkuntho ya Idai

Ofesi ya nthambi ya ku Mozambique yanena kuti nyumba zambiri za abale komanso Nyumba za Ufumu zaonongeka pang’ono ndipo zina zaonongekeratu. Ku Zimbabwe, ofesi ya nthambi yanena kuti nyumba 15 za abale athu komanso Nyumba za Ufumu ziwiri zaonongeka. Ku Malawi, ofesi ya nthambi yati nyumba 764 za abale athu zaonongekeratu ndipo 201 zaonongeka pang’ono. Nyumba za Ufumu ziwiri nazonso zaonongeka. Makomiti Othandiza Pangozi Zadzidzidzi awiri akhazikitsidwa ku Mozambique, pomwe ku Malawi kwakhazikitsidwa makomiti 4 kuti ayendetse ntchito yopereka thandizo.

Mitengo ikuchirikiza madenga a nyumba za abale awiri zomwe zinagwa ku Malawi.

Tili ndi chisoni chachikulu chifukwa cha mavuto amene abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi akukumana nawo. Tikupempherera abale athu onse omwe akhudzidwa kuti apitirize kudalira Yehova yemwe angawapatse mtendere.—Aroma 15:13.