Pitani ku nkhani yake

Kumanzere kupita kumanja: Magazini yoyamba ya The Golden Age (1919), magazini yoyamba ya Consolation (1937), magazini yoyamba ya Galamukani! (1946), komanso magazini ya Galamukani! Na. 2 2019 ya pazipangizo zamakono

OCTOBER 1, 2019
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Magazini ya Galamukani! Yakwanitsa Zaka 100

Magazini ya Galamukani! Yakwanitsa Zaka 100

Pa 1 October, 2019, magazini ya Galamukani! inakwanitsa zaka 100. Pa chaka, magazini a Galamukani! oposa 280 miliyoni amafalitsidwa m’zinenero 211. Galamukani! ndi yachiwiri pa magazini omwe amafalitsidwa komanso kumasuliridwa kwambiri padziko lonse ndipo yoyamba ndi magazini ya Nsanja ya Olonda.

M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira anati: “Galamukani! yachititsa anthu ambiri kukhala ndi chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo chifukwa cha nkhani zosiyanasiyana zomwe imafotokoza. Ngakhale kuti kuchokera pamene inayamba kufalitsidwa yakhala ikusintha kaonekedwe komanso zinthu zina, magaziniyi ikadali chida chothandiza kwambiri pa ntchito yathu yolalikira. N’zosangalatsa kuti yakwanitsa zaka 100 ndipo umenewu ndi umboni wakuti Mulungu akutithandiza ndi mzimu wake woyera.”

Poyamba, a Mboni za Yehova analengeza za kutulutsidwa kwa magazini yotchedwa The Golden Age, womwe unali mutu woyamba wa Galamukani! pa msonkhano wosaiwalika womwe unachitikira ku Cedar Point, Ohio, U.S.A., mu September 1919. Mu 1937, dzina la magaziniyi linasinthidwa kukhala Consolation, n’cholinga choti anthu azimva uthenga wotonthoza. Pomaliza, mu 1946 dzina la magaziniyi linasinthidwanso kukhala Galamukani! pofuna kuthandiza anthu kuti azimvetsa zomwe Baibulo limanena zokhudza zimene zikuchitika padzikoli.

Pa 11 August, 1946, anthu omwe anapezeka pamsonkhano wa Mboni za Yehova mumzinda wa Cleveland ku Ohio anyamula magazini ya Galamukani! yomwe yangotulutsidwa kumene

Tikusangalala kuti takwanitsa zaka zonsezi pamene tikupitiriza kugwiritsa ntchito Galamukani! pa ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo, ‘pochitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.’—Machitidwe 20:24.