Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 11, 2019
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

JW Broadcasting Yakwanitsa Zaka 5

JW Broadcasting Yakwanitsa Zaka 5

Kwa zaka 5 zapitazi, abale ndi alongo padziko lonse akhala akusangalala kuonera pulogalamu ya JW Broadcasting mwezi uliwonse. Pamene tikuyembekezera mapulogalamu omwe akonzedwa mu chaka cha utumiki cha 2020 ndi m’tsogolo, taonani zinthu zina zochititsa chidwi zimene takwanitsa kuchita kungoyambira pamene pulogalamu yoyamba inaulutsidwa mu October 2014.

Ikumasuliridwa m’zinenero 185. Poyamba pulogalamuyi inkaulutsidwa m’Chingelezi mokha. Kenako mu May 2015, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti pulogalamuyi izimasuliridwa m’zinenero zina zoposa 40. Pofika pano, ikumasuliridwa m’zinenero 185 pa avereji.

Ikuthandiza anthu padziko lonse. Popeza kuti cholinga cha pulogalamuyi ndi kuthandiza abale ndi alongo padziko lonse lapansi, mavidiyo ambiri omwe amaonetsedwa amajambulidwa ndi magulu a abale ndi alongo opanga mavidiyo m’mayiko osiyanasiyana. Nthawi zambiri kumapeto kwa pulogalamu ya JW Broadcasting iliyonse kumakhala kavidiyo kosonyeza mipingo ya m’madera akutali kuphatikizapo madera a ku Ethiopia, Iceland, Mongolia, Saipan, Tuvalu, ndi Uganda. Anthu a m’mayiko 230 akhala akuonera pulogalamuyi kuphatikizapo anthu a m’madera a kumidzi monga kuzilumba za kum’mwera kwa dziko lapansi ku Heard Island ndi ku McDonald Islands komwe anthu sakhazikikako. Pa avereji, m’mwezi womwe pulogalamu yatsopano yatuluka, imaoneredwa kapena kupangidwa dawunilodi maulendo pafupifupi 8.6 miliyoni.

Ili ndi zinthu zambiri zosiyanasiyana. Pali mavidiyo a zinthu monga nkhani, kufunsa mafunso, zochitika pa moyo, nkhani zatsopano, ndi masewero ndipo zonsezi ndi za maola oposa 60. Kungoyambira pamene nyimbo yoyamba yakuti Moyo Wabwino Kwambiri inatuluka, nthawi zambiri pa JW Broadcasting pamatulutsidwa vidiyo ya nyimbo. Nyimbozi zimamasuliridwa m’zinenero 368.

Amene amachititsa pulogalamuyi. Poyamba, abale a m’Bungwe Lolamulira okha ndi amene ankachititsa JW Broadcasting iliyonse. Kenako, abale othandiza m’makomiti a Bungwe Lolamulira ankathandiza ndipo nthawi zina ankachititsa pulogalamuyi. Pofika pano, abale osiyanasiyana omwe achititsa kapena kuthandiza kuchititsa pulogalamu mwezi ndi mweziyi alipo 29.

Zimene Ena Ananena. M’bale wina wa ku United States yemwe anadwalapo sitiroko ndipo amavutikabe chifukwa cha matendawa amayamikira kwambiri nyimbo za pa JW Broadcasting. Iye anati: “Nyimbozi n’zothandiza kulimbitsa chikhulupiriro mwa Yehova ndi Mawu ake ndipo zandithandiza kuti ndiziona zinthu moyenera ndi kupirira matenda angawa. Ndazindikira kuti nyimbozi zandithandiza kwambiri kukhala ndi makhalidwe abwino Achikhristu. Zikomo kwambiri chifukwa cha nyimbo zimenezi.”

Pambuyo poonera JW Broadcasting ya November 2016, banja lina la ku United States lomwe mwana wawo wamwamuna anamwalira atadwala matenda a khansa linalemba kuti: “Tinagwetsa misozi pamene tinkaonera vidiyo ya nyimbo yakuti Dziko Latsopano Lili Pafupi. Tinkangomva ngati ifeyo ndi makolo omwe amaonetsedwa muvidiyo ya nyimboyi ali m’paradaiso. Tikayamba kuganiza zoti sitingathe kupirira nkhawa zomwe tili nazo, Yehova amatithandiza kudziwa kuti amamvetsa komanso atithandiza kupirira. Vidiyoyi inali ngati yankho lochokera kwa Yehova pa mapemphero athu ambiri ochokera pansi pamtima.”

Banja lina la ku Ukraine linayamikira mapulogalamu a mwezi ndi mweziwa, ndipo linati: “Tikuthokoza kuti JW Broadcasting yatithandiza kuwadziwa bwino abale a m’Bungwe Lolamulira ndipo timawaona monga anthu a m’banja lathu.”

Tikuyamikira Yehova chifukwa cha pulogalamu ya pa nthawi yake imeneyi yomwe ikupitiriza kuthandiza kuti anthu ake azigwirizana padziko lonse.—1 Petulo 2:17.