Lachisanu pa 18 May, 2018, ndege ya Boeing 737 inagwa itangonyamuka kumene mumzinda wa Havana, ku Cuba. Pa anthu 113 omwe anali mu ndegeyi, munthu mmodzi yekha ndi amene anapulumuka ndipo kwa zaka zambiri, palibe ngozi yandege yoopsa kwambiri yomwe inachitika m’dzikoli kuposa imeneyi.

N’zomvetsa chisoni kuti a Mboni za Yehova atatu a m’banja limodzi (bambo, mayi ndi mwana wamwamuna wa zaka 22), anali m’gulu la anthu omwe anafa pangoziyi. Iwo anali akhama mumpingo mwawo ku Cuba ndipo abale ndi alongo ankawakonda. Mwambo wa maliro wa banjali unachitika Loweruka pa 26 May, 2018.

Akulu a mumpingo m’deralo akuthandiza komanso kutonthoza achibale ndi anzawo a omwalirawo pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo ndipo nawonso akuluakulu a boma m’deralo anapereka chithandizo. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza ‘kutonthoza anthu onse olira’ pa nthawi yovuta imeneyi.—Yesaya 61:1, 2.