Pitani ku nkhani yake

Akaidi akuphunzira Baibulo kundende ya Barranquilla.

APRIL 26, 2019
COLOMBIA

A Mboni za Yehova ku Colombia Alandira Satifiketi Yowayamikira Chifukwa cha Ntchito Yophunzitsa Akaidi Baibulo

A Mboni za Yehova ku Colombia Alandira Satifiketi Yowayamikira Chifukwa cha Ntchito Yophunzitsa Akaidi Baibulo

Satifiketi yochokera ku Paulo Freire Educational Center yoyamikira ntchito yophunzitsa Baibulo yomwe ikuthandiza akaidi kundende ya Valledupar.

Kwa zaka zoposa 20, abale athu ku Colombia akhala akuphunzitsa akaidi Baibulo kwaulere. Pa 30 November, 2018, a Mboni anapatsidwa satifiketi kuchokera ku Paulo Freire Educational Center powayamikira chifukwa chogwira ntchito yophunzitsa Baibulo kundende ya mumzinda wa Valledupar. Panopa akaidi 50 a kundendeyo amaphunzira Baibulo.

M’dziko la Colombia, a Mboni za Yehova amaphunzitsa akaidi Baibulo m’ndende 65 ndipo amachititsa maphunziro a Baibulo 782. Kuyambira mu 1996, anthu okwana 60 aphunzira Baibulo mpaka kufika pobatizidwa.

A Néver Antonio Cavadía anaphunzira Baibulo ali m’ndende ndipo panopa akutumikira monga mkulu. M’chithunzichi, ali limodzi ndi mkazi wawo Lety Cavadía.

A Néver Antonio Cavadía anaphunzira Baibulo ali m’ndende ndipo anabatizidwa mu 1998. Kenako anatulutsidwa m’ndende ya Valledupar mu 2007. Pofotokoza mmene kuphunzira Baibulo kunawathandizira, iwo anati: “Mfundo za m’Baibulo zinanditeteza komanso zinandithandiza kuti ndizichita zinthu mwanzeru pa nthawi yomwe ndinali m’ndende. Zinandilimbikitsanso kuti ndisinthe kwambiri moyo wanga komanso kukhalabe ndi chiyembekezo.”

Kuzungulira padziko lonse, a Mboni za Yehova timayesetsa kulalikira kwa akaidi chifukwa timadziwa kuti zimenezi n’zogwirizana ndi cholinga cha Yehova choti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Timoteyo 2:4.