Pitani ku nkhani yake

Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo ku Bulgaria, mumzinda wa Sofia

MAY 20, 2019
BULGARIA

Milandu Yomwe a Mboni za Yehova Awina ku Bulgaria Ikuteteza Ufulu Wawo Wopembedza

Milandu Yomwe a Mboni za Yehova Awina ku Bulgaria Ikuteteza Ufulu Wawo Wopembedza

Mu March 2019, Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo ku Bulgaria, lomwe ndi lamphamvu kwambiri m’dzikoli, linagamula milandu itatu yokhudza abale athu mowakomera. Zigamulozi n’zofunika kwambiri chifukwa zithandiza kuti makhoti ena onse m’dzikolo azilemekeza ufulu wolambira wa abale athu.

Milandu iwiri inali yokhudza zinthu zabodza zoneneza a Mboni zomwe zinafalitsidwa ndi nyuzipepala komanso wailesi ina yakanema. Mu 2012, nyuzipepala ya Vseki Den inafalitsa nkhani yonama yokhudza zikhulupiriro zathu. Chimodzimodzinso mu 2014, wailesi yakanema ya SKAT TV inaulutsa lipoti labodza lokhudza gulu lathu. Magulu ofalitsa nkhani awiriwa anakana abale athu atawapempha kuti alengeze kuti zinthu zomwe anafalitsazo zinali zabodza. Pambuyo pokadandaula za nkhaniyi ku makhoti komanso atapanga apilo maulendo angapo, milanduyi inakafika ku Khoti Lalikulu Kwambiri. Pa 18 March, 2019, Khoti Lalikulu Kwambiri linagamula kuti zimene wailesi yakanema ya SKAT TV inachita n’zosemphana ndi malamulo. Pa 26 March, Khotili linagwiritsa ntchito chigamulo chimenechi pa mlandu wa nyuzipepala ya Vseki Den ndipo linadzudzula a nyuzipepalayi kuti zomwe analemba zinali zonama komanso zinasonyeza kuti akudana ndi a Mboni.

Mlandu wachitatu unali wokhudza nkhanza zomwe gulu la chipani lotchedwa VMRO-Bulgarian National Movement linachitira abale athu. Pa 17 April, 2011, abale athu anasonkhana kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Kenako gulu la anthu achiwawa omwe analipo 60, lomwe linatumidwa ndi mtsogoleri wa VMRO dzina lake Georgi Drakaliev, linafika mwachiwawa n’kuvulaza abale athuwa. Abale anapita ku makhoti kukadandaula za nkhaniyi. Kenako nkhaniyi inakafika ku Khoti Lalikulu Kwambiri. Pa 20 March, 2019, khotili linagamula kuti bambo Drakaliev ndi olakwa ndipo panopa ayenera kulipira abalewa.

Tikusangalala chifukwa cha zigamulo zitatu zokomera abale athuzi. Tsopano makhoti akhoza kumagwiritsa ntchito zigamulozi akamazenga milandu ina poteteza ufulu wa abale athu kuti ‘akhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti akhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira.’—1 Timoteyo 2:2.