Pa 31 October, 2018, Khoti la Apilo mumzinda wa Ganja ku Azerbaijan linapereka chigamulo chofanana ndi chomwe khoti lina laling’ono linapereka choti m’bale Vahid Abilov wazaka 19, ndi wolakwa pa mlandu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ngakhale kuti m’bale Vahid sanaikidwe m’ndende, koma anapatsidwa malamulo a zinthu zomwe ayenera kuchita komanso zomwe sayenera kuchita kwa chaka chimodzi. Mwachitsanzo, analamulidwa kuti mlungu uliwonse azikaonekera kupolisi komanso asatuluke m’dziko la Azerbaijan. Vahid akachita apilo ku Khoti Lalikulu Kwambiri ku Azerbaijan ndipo limeneli ndi khoti lomaliza m’dzikolo lomwe akuyembekezera kuti lingaweruze nkhani yake mwachilungamo.

M’bale Abilov anayamba kukumana ndi mavutowa kuyambira mu May 2017. Pa nthawiyi, anali atangokwanitsa kumene zaka 18 ndipo ankafunika kukalembetsa ku dipatimenti ya boma yomwe imalemba anthu ntchito ya usilikali m’tawuni ya Aghdam. Koma m’baleyu analemba kalata yofotokoza kuti sangagwire ntchito yausilikali. Iye analemba kuti: “Chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo sichindilola kulowa usilikali. Sikuti ndikukana kuthandiza dera langa kapena kuzemba udindo wanga wothandiza dziko langa monga nzika ya dziko la Azerbaijan. Ndikungopempha kuti mundipatse ntchito ina m’malo mwa usilikali.” Akuluakulu a boma anakana pempho la Vahid ndipo pa 9 July, 2018, anamupeza wolakwa pa mlandu wozemba ntchito yausilikali.

Pa nthawi yomvetsera mlanduwu mu Khoti la Apilo ku Ganja, m’bale Abilov anapitiriza kufotokoza chifukwa chake akukanira ntchito yausilikali. Iye anawerenga lemba la Yesaya 2:4 m’khotimo ndipo anafotokoza kuti kufufuza bwino mfundo za m’Baibulo kunamuthandiza kuzindikira kuti “sakuyenera kuphunzira kumenya nkhondo.” Koma ngakhale kuti anafotokoza zimenezi, khotilo linanenabe kuti wolakwa. Tikuyembekezerabe kuti tione ngati Khoti Lalikulu Kwambiri lilemekeza zimene m’baleyu akufuna zoti apatsidwe ntchito zina m’malo mwa usilikali.

Dziko la Azerbaijan litakhala membala wa Bungwe la Mayiko a ku Europe mu 2001, linanena kuti likhazikitsa lamulo lomwe lizipatsa anthu ufulu wogwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Koma bomali silinakhazikitsebe lamuloli. Chifukwa cha zimenezi, abale athu nthawi zonse amakumana ndi mavuto akakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Chakumayambiriro a chaka chino, khoti la m’boma lina ku Azerbaijan linagamula kuti mmodzi mwa abale athu, dzina lake Emil Mehdiyev, ndi wolakwa chifukwa chozemba ntchito yausilikali ndipo anamulamula kuti azikaonekera kupolisi kwa chaka chimodzi. A Mehdiyev nawonso anapanga apilo za nkhaniyi ku Khoti Lalikulu Kwambiri. Kuonjezera pamenepa, tikuyembekezera zomwe Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe ligamule pa milandu ya abale athu 4 amene anakana kulowa usilikali ku Azerbaijan. Ngakhale kuti abale athu akukumana ndi mavutowa, iwo akupitiriza kudalira Yehova kuti asakhale mbali ya dziko.—Yohane 15:19.