Pitani ku nkhani yake

Anthu othawa kwawo omwe amakhala ku kampu ya Lóvua ali pamsonkhano wadera wa Chitchiluba

SEPTEMBER 12, 2019
ANGOLA

Misonkhano Yadera Inachitika Kukampu ya Anthu Othawa Kwawo M’zinenero za Chilingala ndi Chitchiluba ku Angola

Misonkhano Yadera Inachitika Kukampu ya Anthu Othawa Kwawo M’zinenero za Chilingala ndi Chitchiluba ku Angola

Pa 25 ndi 26 May, 2019, msonkhano wadera wakuti “Muzichita Zinthu Mwamphamvu” wa m’zinenero za Chilingala ndi Chitchiluba, unachitikira ku kampu ya anthu othawa kwawo ya Lóvua. Kampuyi ili pamtunda wamakilomita 1,022 kuchokera mumzinda wa Luanda womwe ndi likulu la dziko la Angola. Pa nthawi yomwe msonkhanowu unkachitika, ku kampu ya Lóvua kunkakhala ofalitsa 177 pamodzi ndi mabanja awo. Ngakhale zili choncho, anthu okwana 380 anapezeka pa msonkhano wa Chilingala ndipo anthu atatu anabatizidwa. Pamsonkhano wa Chitchiluba panapezeka anthu 630 ndipo anthu 6 anabatizidwa.

Abale ambiri omwe ali ku kampu ya Lóvua anathawa kwawo chifukwa cha zachiwawa zomwe zinkachitika ku Democratic Republic of the Congo. Abale athu ku Lóvua sangakwanitse kupita m’mizinda ina kuti akachite misonkhano chifukwa choti anthu omwe amakhala ku kampu amaletsedwa kupita m’madera ena. Choncho, ofesi ya nthambi inakonza zoti misonkhano ichitikire ku kampuyi ndiponso inamanga Nyumba za Ufumu ziwiri zongoyembekera. Mipingo 4 ndi imene imachitira misonkhano m’Nyumba za Ufumu zimenezi, itatu ya Chitchiluba komanso umodzi wa Chilingala.

Pa 24 May, 2019, woyang’anira dera limodzi ndi woimira ofesi ya nthambi anapita ku kampu ya Lóvua kuti akathandize kulumikiza zokuzira mawu komanso zinthu zogwiritsa ntchito ku pulatifomu. Ngakhale kuti abale athu akukumana ndi mavuto chifukwa chothawa kwawo, abalewa anathandiza popereka zinthu monga malona, mitengo, chingwe, misomali ndi zinthu zina zomwe zinkafunikira.

Msonkhanowu utatha, a Honoré Lontongo omwe ndi mtumiki wothandiza mumpingo wina wa Chitchiluba ku kampu ya anthu othawa kwawo anati: “Kuona misonkhanoyi ikuchitikira mu kampu ya anthu othawa kwawo ngakhale tikukhala movutikira, zikutithandiza kudziwa kuti Yehova amatikonda osati monga gulu basi koma aliyense payekha. Ndasangalala kwambiri!”

Tipitiriza kupempherera abale athu omwe anathawa kwawo chifukwa cha mavuto a zandale amene akuchitika padzikoli. Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kupereka chakudya chauzimu komanso zinthu zofunika kwa abale athu kulikonse komwe ali.—Aroma 8:38, 39.

 

Abale akumanga pulatifomu komanso kulumikiza zokuzira mawu

Anthu omwe akuyembekezera kubatizidwa aimirira kuti ayankhe mafunso aubatizo pamsonkhano wadera wa Chitchiluba

Abale ndi alongo olankhula Chilingala akupita kumtsinje womwe uli pamtunda wamakilomita awiri kuchokera ku kampu kuti akaonerere ubatizo

M’bale Johannes De Jager wa m’Komiti ya Nthambi, ali limodzi ndi abale ndi alongo olankhula Chilingala msonkhanowu utatha