Pitani ku nkhani yake

Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova

Werengani nkhani zokhudza Mboni za Yehova pa intaneti. Palinso nkhani zothandiza akatswiri a zamalamulo komanso ofalitsa nkhani.

UKRAINE

A Mboni za Yehova ku Ukraine Anaonetsa Anthu Mabaibulo M’malo Osiyanasiyana

A Mboni za Yehova ku Ukraine anachita zionetsero zapadera za Baibulo pofuna kudziwitsa anthu za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero Chamanja cha ku Russia.

ITALY

Madokotala ku Italy Anasonyeza Chidwi pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi

Misonkhano iwiri imeneyi inathandiza kuti akatswiri ambiri azachipatala adziwe njira zatsopano zokhudza kuthandiza odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi. Komanso, madokotala opanga maopaleshoni anafotokozera abale ndi alongo zinthu zabwino zomwe akhala akukumana nazo akamagwira ntchito ndi a Mboni za Yehova.